Chichewa

Ntchito za Kumbu Kalipo (KK)

Listen to this article

Tsikulo pa Wenela padaterera ndithu. Aliyense adali ndi chodzala tsaya chimwemwe. Sindikudziwa kuti zidali choncho chifukwa chiyani.

Komatu ngakhale kudali chimwemwe chotero, inetu msunamo udali kuno. Ndidali kudandaula chifukwa mmodzi mwa anthu amene adandilandira pano pa Wenela adali atatsamira mkono. Iyetu ndi amene nthawi ina ankandiphunzitsa kukonza galimoto. Ndipo tsiku lomaliza, adandiuza ndikamuthandize kukonza galimoto kuti tikaone zina uko kwa Edgar Lungu, mtsogoleri wothamanga.

TADEYO

Lero wapita.

Pajatu ati moto umapita kwatsala tchire. Pamene tikuyembekeza kuti iye akhale mchiyero, malingaliro ali pa ife otsala.

Ause ndi mtendere.

Choncho, monga ndanena kale, chimwemwe chidali pa Wenela inetu sichinkandikhudza. Koma ndidazizwa atatulukira KK, inde Kumbukani Kalipo, sikanathe.

“Nonse amene mumachokera ku Northern Republic, inde Nyika Province, nthawi yanu yakwana. Tipeza mipando ndipo onse obulumunya maswiti polankhula, okazinga chimanga, nthawi yawo yatha kwambiri. Ndabwerera,” adatero Kumbu.

Abale anzanga, ngati ndidatolapo kanthu?

“Nthawi yanu idatha. Ngakhale muyese izi ndi izo, zanu zidada basi,” adatero Abiti Patuma.

Adandikulunga m’masamba ansatsi.

“Usatero mwaiwe. Ukudziwa Adona Hilida akabwera kumakhala mpungwepungwe. Anabweratu ndipo tagwirizana zosadabuza zinthu pano pa Wenela,” adayankha Kumbu.

Mwinatu muli ngati mkazi wanga Nambe kuti simudziwa umo zinthu zikuyendera pano pa Wenela.

Kulitu kusankha, inde masankho. Dizilo Petulo Palibe, Polisi Palibe, Male Chauvinist Pigs ngakhalenso Ukafuna Dilu Fatsa akufuna kuonetsa kuti wamphamvu ndani.

Adatulukiranso Adona Hilida. Adanong’oneza Kumbu kukhutu.

“Iwe, masewera ayi. Ukapanda kutenga mipando, yako ntchito yatha zenizeni. Tapita ukatenge mipando,” adatero Adona Hilida.

Adapitiriza: “Kaya unama kuti wandilanda mpando; kaya unena kuti sunandilande, izo ndi zako. Koma utenge mpando. Pajatu Angoni a Chitumbuka ngati iwe ntchito zanu nzoopsa.”

“Nditero dona. Kodi uyu, Mzome, nambala yake muli nayo? Andimveke ufumu wanu basi. Kaya ndiutenga kaya sindiutenga, zonse adziwa ndi Ambuye,” adatero Kumbu.

“Komatu mukunamizana. Dikirani ndimuuze Koko Wakhuma zomwe mukukambirana,” adatero Abiti Patuma.

Adaika foni yake pa loud kuti ndizimva.

“Imeneyo isiye kaye. Iyo ndi nkhani yotentha. Nkhani yonona. Koma ndili kaye ku Ginnery Corner. Ndikufuna n’tamudziwa Tadeyo,” adatero Koko.

Uyo sanagwire bango, ndithu shuwa apita ndi madzi. Nthawi yatha.n

Related Articles

One Comment

Back to top button
Translate »