Nkhani

Ntchito za wedewede zanyanya

Listen to this article

Kusowa ndalama zoyendera zitukuko komanso kulekera anthu a kumudzi kugwira ntchito zomangamanga zachitukuko kukuchititsa kuti ntchitozi zizikhala zawedewede, atero akadaulo ena.

Izi zikudza patangotha sabata imodzi chipinda cha sukulu ya pulaimale ya Natchengwa ku Zomba chitagwa ndi kupha ophunzira 4 ndi kuvulaza ena. Mwezi watha, mlatho wina udadilizika galimoto ina ikudutsa ndipo anthu akhala akugawana zithunzi za msewu wosalongosoka mumzinda wa Lilongwe.

Zipinda za ku Nantchengwa zzidamangidwa ndi dothi

Komiti ya zomangamanga ku Nyumba ya Malamulo ili ndi mphamvu zoyang’anira ndi kuunikira pa momwe nyumba, misewu kapena milatho zikumangidwira kuti zizikhala zapamwamba ndi zolimba.

Koma wapampando wa komitiyo, Victor White Mbewe adati nthawi zambiri komitiyi imalephera kukwaniritsa ntchitoyi chifukwa imalandira thumba losakwanira kuzungulira dziko lonse kuyendera zitukuko.

“Tikadakhala kuti timalandira thumba lokwanira, si bwenzi iyi ili nkhani chifukwa bwenzi tikumayenda paliponse kukaona momwe zitukuko zikuyendera. Zitukuko zambiri zikumangidwa ndi anthu akudera osayenderedwa,” adatero Mbewe.

Mkulu wa bungwe la akatswiri a zomangamanga la Malawi Institute of Architects Mariam Mdooko wavomeleza kuti vuto lalikulu ndi loti nyumba zambiri zimamangidwa osafunsa ukadaulo wa ozidziwa.

“Pali sukulu, zipatala, malo a bizinesi ndi nyumba zina zimene zikumangidwa osatsata ndondomeko. Ife akadaulo timadziwa zofunika ndi mamangidwe

ake koma nthawi zambiri zimangomangidwa osatifunsa,”

adatero Mdooko.

Iye adati njira yokhayo yothanirana ndi vutoli n’kuonetsetsa kuti ntchito yomanga isadayambike, akadaulo kaya a pakhonsolo kapena a mabungwe akuluakuluwa azifunsidwa.

Mneneri wa bungwe loyang’anira ntchito zomangamanga m’dziko muno la National

Construction Industry Council Laison Gideon adati nthambiyo ili ndi malamulo omwe amayenera kutsatidwa kuchokera pachiyambi mpaka kumapeto.

“Malamulo athu amati kontilakitala aliyense akuyenera

kulembetsa m’kaundula wathu. Ndipo ntchito iliyonse isadayambe tiuzidwe kuti tizitha kuyilondoloza ndipo timatero,” adatero Gideon.

Iye adati ndondomeko izi sizitsatidwa nthawi zambiri chifukwa anthu ena amafuna kupanga zozemba koma sadziwa kuti zotsatira zake zimakhala zovuta ngati zomwe zimawonekazi.

Gulupu Matabwa, kwa T/A Chitekwere ku Lilongwe adati aphungu ndi makhansala amaika dyera ndi ndale patsogolo, zomwe zimadzetsa zitukuko zawedewede, zomwe zimathera m’ngozi ngati ya ku Zomba. Iye adati nthawi zina adindowa amadza ndi kontilakita wawowawo, mosemphana ndi amene komiti yachitukuko idasankha.

“Komiti imatha kugwirizana wodzagwira ntchito ya chitukuko koma nthawi ikakwana, timangoona akubweretsapo munthu wawo. Timangozindikira katundu wafika ndipo ayamba kugwira ntchito,” idatero mfumuyo.

Mkulu a bungwe loona kuti maphunziro ndi apamwamba, la Civil Society Coalition for Education (CSCE) Benedicto Kondowe wati kafukufuku wawo adapeza madera ambiri omwe anthu amadandaula kuti aphungu awo amawabweretsera kontilakitala komanso kuwagulira zipangizo osawafunsa maganizo awo.

Mlembi wamkulu muunduna wa za maboma ang’onoang’ono ndi chitukuko cha m’midzi Kiswell Dakamau adati mundondomeko ya mphamvu ku anthu, boma lidakhazikitsa ndondomeko ya momwe akadaulo aboma aziyang’anira momwe zitukuko zikuyendera ndipo izi zikutheka.

Iye adati akati mphamvu ku anthu amangofuna kuti eni dera azitengapo mbali posankha chitukuko, kupeza malo komanso kuchita kalondolondo wa momwe ndalama zachitukuko cha m’dera lawo zikugwirira ntchito.

“Zinthu zikuyenda m’madera ambiri ndipo kunena kuti boma limalekerera anthu a kumudzi sizoona chifukwa chitukuko chilichonse chomwe chalowa m’mabuku athu, chimakhala ndi wochiyang’anira pokhapokha ngati

sitikuchidziwa,” adatero Dakamau.

Mkulu wa bungwe loyang’anira za misewu Emmanuel Matabwa adati potsitira mgwirizano wa maiko a Sadc, nthambiyi idasintha kasankhidwe ka makontirakitala ndi kuunika ntchito.

“Panopa kulibe zawedewede chifukwa tidamanga mabauti kuyambira pakasankhidwe ka makontilakitala, kuwapatsa mlingo omwe tikufuna ndi kuunika kuti akutsatiradi zomwe tawauzazo,” adatero Matabwa.

Iye adati chitsanzo cha misewu yotere ndi wa Mzuzu-Nkhatabay omwe uli ndi milatho yolimba komanso ndi wotakasuka ndi wopsinjidwa bwino kuti usadzaonongeke msanga.

Related Articles

Back to top button