Chichewa

Nthula: Abambo ofooka kuchipinda achangamuke

Listen to this article

Akuti abambo ena amafooka pamene akucheza ndi akazi awo chifukwa cha zina zomwe zimasowekera pamene machezawa ali mkati. Ichi nchifukwa chake makolo akale amakhulupirira kuti pakhale nthula kapena kuti mthunduwere zomwe zimachangamutsa amuna oterewa. Ibra Monjeza wa m’mudzi mwa Sauka kwa T/A Malemia m’boma la Zomba ndiye akufotokoza izi kwa BOBBY KABANGO.

 

Monjeza kufotokozera anthu za kufunikira kwa nthunduwere
Monjeza kufotokozera anthu za kufunikira kwa nthunduwere

Tidziwane bwinobwino….

Ine ndi Monjeza, ndine mlimi komanso anthu amandidziwa bwino ndi ulangizi wanga. Ulangizi wokhudza mabanja komanso ulimi.

Ndi ulangizi wanji omwe mutipatse lero?

Ndikupatsani ulangizo omwe ndimawafotokozera anthu pafupifupi tsiku lililonse. Uwu ndi ulangizi kwa amayi zomwe ayenera kuchita kuti bambo asamafooke pamene akucheza nawo.

Ndiye amayenera atani?

Nkhani ndi nthula basi. Kugwiritsa ntchito nthula molondola ndiye kuti zako zayera, bambo abwekera nthawi zonse ndipo sangafooke.

Nthula nchiyani?

Ndi zibalobalo za kamtengo kakang’ono kamene kamakhala ndi minga. Ena amati nthunduwere ndipo mbuzi zimadyanso.

Mwati zimathandiza chiyani?

Dziwani kuti macheza pakati pa bambo ndi mayi amakhalabwino ngati aliyense akusangalala. Bambo amakhala nthawi yaitali pamene akucheza ndi mayi ngati mayiyo wapanga zomusangalatsa. Apa ndi pamene tikuti nthula zimagwira ntchito kuti machezawa akhale a nthawi.

Nthula ndiye zimapanga chiyani?

Zimakometsera machezawo. Kuti athe nthawi pakufunika nthula kuti nonse awiri akhutitsidwe.

Mumazitani nthulazo kuti zifike pamenepa?

Umafunika uthyole nthulayo koma usankhe yoti ikupita koola, imakhala yoti ili biii! kuda. Dziwani kuti amayi ndiwo amagwiritsira ntchito nthulayi osati amuna. Imangopangitsa kuti mwamuna asangalale pamene akucheza.

Ndiye munthu wa mayiyo atani akatenga nthulayo?

Amaying’amba pakati ndi kumagwiritsira ntchito. Pakutha pa sabata mayiyo amakhala wasinthiratu, akati acheze ndi mwamuna zimakhala zabwino chifukwa mwamuna amasangalala ndithu.

Amazigwiritsa bwanji ntchito ndipo chimathekacho nchiyani?

Akangoyicheka pakati nthulayo, basi apite kwa mayi aliyense amene ndi wamkulu m’dera lawo ndipo akamuuza bwino momwe angaigwiritsire ntchitomo. Akaigwiritsa ntchito bwino, amakhala mkazi woti mwamuna amasangalala naye pamene akuchita macheza ndipo ngakhale amuna ofooka amalimbikitsidwa.

Tafotokozani bwino.

Sindinena. Dziwani kuti kale mtundu ulionse umadziwika ndi zochita zake. Angoni, Achewa ndi ena timawadziwa momwe akuchitira kuchipinda koma masiku ano aliyense amatsata njira zomwe akufuna kuti asangalatse amuna ake. Kale Alhomwe timawadziwa ndi mikanda, koma lero upezanso ena omwe ndi Alhomwe alibe mikanda. Izitu zikusonyeza kuti chikhalidwe chidasokonekera ndipo aliyense akupanga chomwe akufuna. Izi ndikunenazi ndi zachikhalidwe ndiye sindinganene wamba.

Osati mukungotinamiza apa?

Kodi inu mudakwatira? Kapena mudayambapo mwacheza ndi mayi ndipo mudasiyanitsapo? Chifukwa ngati mudachitapo izi, bwezi mutandimvetsa. Sindikunama, izi ndi zoona.

Inuyo mudasiyanitsapo?

[Akuseka….] ndikudziwa chomwe ndikunena.

Related Articles

Back to top button