Nkhani

Nyumba ya Malamulo yakhutira ndi MEC

Listen to this article

Komiti yolondoloza malonjezo a boma ku Nyumba ya Malamulo yati ndiyokhutira ndi lipoti la bungwe loyendetsa zisankho la Malawi Electoral Commission (MEC).

Bungwe la MEC lidawonekera pamaso pa komitiyo Lachiwiri m’sabatayi kukapereka lipoti la momwe zokonzekera za chisankho chapatatu zikuyendera.

Alfandika: Tili ndi masiku 7 ofufuza atsogoleri

Polankhula ndi Tamvani, wapampando wa komitiyo Yaumi Aufi Mpaweni adati lipoti la MEC likusonyeza kuti ntchito yokonzekera chisankho ikuyenda bwino ndipo komiti yonse idagwirizana ndi zomwe idawona ndi kumva kuchoka ku MEC.

“Tidayitana bungwe la MEC kuti lidzatipatse lipoti. Zomwe adatiuza zikusonyeza kuti ntchito ikuyenda bwino ndipo mamembala onse akomiti adakhutira ndi lipotiro. Ngati kungawoneke zovuta, tiwona mtsogolomu,” adatero Mpaweni.

Iye adati komitiyo ndiyokonzeka kuthandizira pomwe bungwe la MEC lingakumane ndi zovuta za mtundu uliwonse pofuna kuti chisankho cha chaka chino chidzayende mokomera zipani ndi anthu onse.

Mulipoti lake, mkulu woyang’anira zisankho ku bungwe la MEC, Sam Alfandika adafotokoza momwe ntchito za kalembera, kuunika maina, kupeleka zikalata za ofuna kudzapikisana nawo pamipando ya mtsogoleri wa dziko ndi wachiwiri wake komanso aphungu ndi makhansala zidayendera.

Iye adalongosolanso zovuta zomwe akuyembekezera ndi ndondomeko zomwe bungwelo lakonza zofuna kudzathana ndi zovutazo zitadzawoneka.

“Monga mukudziwa, anthu adalembetsa 6 859 570 pogwiritsa ntchito njira yamakono yomwe idatithandiza kuchepetsa chinyengo. Padali chiseso chochotsa maina opezeka kangapo mkaundula ndipo maina 13 244 adachotsedwa,” adatero Alfandika.

Iye adati pozindikira kuti kunja kuli akathyali malinga ndi makono, bungwelo lidapeza akadaulo a nkhani za zida zamakono omwe azithandizira kuwonetsetsa kuti palibe yemwe walowerera chinsinsi cha bungwelo.

Alfandika adauzaso komitiyo kuti amene akufuna kupikisana nawo adapeleka kalata zowonetsa zolinga zodzapikisana nawo ndipo adati ntchitoyo idayenda bwino.

“Tidalandira zikalata zonse koma tikuziunikabe moti pakutha kwa masiku 7, tikhala tikutulutsa maina omalizira omwe tawavomereza kudzapikisana nawo pa mpando wa mtsogoleri wa dziko lino. Pamene ntchito younguza aphungu a Nyumba ya Malamulo idzatenga masiku 14. Ndipo makhansala itenga masiku 21,” adatero Alfandika.

Iye adatsimikizira komiti ya aphunguyo kuti bungwe la MEC likufufuza makampani omwe adzasindikize zipangizo zoponyera voti. na

Related Articles

Back to top button