Nkhani

Obera malova akuchuluka

Listen to this article

Akapsala obera achimata amapepala awo powalonjeza ntchito zomwe chikhalirecho palibepo akuchulukirabe m’mizinda ngakhale kuti apolisi ndi unduna wa zantchito akulimbana ndi mchitidwewu.

Kumapeto a mwezi wathawu, pa 29 August, apolisi m’boma la Mchinji adagwira Yohane Chimkumbi, wa zaka 32, wa m’mudzi mwa Ndeleya kwa T/A Mamvere pomuganizira kuti adadya ndalama zokwana K87 000 atanamiza achinyamata 6 kuti awalemba ntchito m’bungwe lake, koma adati aliyense ayambe wapereka K10 000.

Wachiwiri kwa mneneri wa apolisi m’bomali, Rome Chauluka, adati mkuluyu akuti adauza achinyamatawo kuti pali bungwe lotchedwa Young Advocacy lomwe likufuna anthu oti liwatumize m’madera osiyanasiyana kukagwira ntchito.

“Munthuyu adangobwera n’kuyamba kuuza achinyamata kuti pali mwayi wa ntchito ndiye mwina ndi ulovawu aliyense akusakasaka mwayi wa ntchito kotero kuti atawauza kuti apereke K10 000 aliyense adangoona ngati mwayi wapezeka,” adatero Chauluka.

“Akuti amati akamufunsa amanena masitetimenti osiyanasiyana monga oti akungodikira mabwana ake kuti amumasule kulemba achinyamatawo koma ataona kuti payamba kutentha, iye adathawa kuderalo,” adatero Chauluka.

Sabata zingapo zapitazo, Tamvani idasokolotsa nkhani ya akamberembere ena omwe amanka m’mizinda kukhoma zikalata zoti akufuna achinyamata omwe akusowa ntchito koma atafufuza adapeza kuti nkhani yake idali yomweyi yofuna kuwabera.

Wapampando wa bungwe loyendetsa mabungwe a achinyamata la National Youth Council of Malawi (NYCOM), Aubrey Chibwana adati vutoli lingathe achinyamata atakhala ndi mtima wongogwira ntchito modzipereka ngakhale asadamalize maphunziro awo ndi cholinga choti asadzavutike kupeza ntchito mtsogolo.

“M’maiko ambiri achinyamata amayamba kugwira ntchito mongodzipereka kuti akadzamaliza maphunziro adzakhale ndi umboni woti amadziwa kale ntchitoyo ndipo adaigwirako. Nthawi zina makampani omwe akugwirako ntchito moteromo amatha kungowatengeratu,” adatero Chibwana. n

Related Articles

Back to top button
Translate »