ChichewaFront Page

Obindikira m’nyumba azengedwa mlandu

Listen to this article

 

Bwalo la milandu la majisitireti mumzinda wa Blantyre lakhazikitsa Lachitatu, 25 May, ngati tsiku lomwe lidzapereke chigamulo kwa banja lina lomwe lakhala likudzitsekera m’nyumba kwa zaka zitatu ndi kulephera kupereka chisamaliro kwa ana awo anayi.

Mneneri wa nthambi ya zachilungamo, Mlenga Mvula watsimikizira Msangulutso za nkhaniyi.

Mvula adati nkhaniyi idalowa m’khoti pa 13 May ndipo banjali lidakana mlandu wolephera kupereka chithandizo kwa ana awo ndipo ilowanso m’bwaloli Lachitatu likubwerali pa 25 May pamene oimira boma abweretse mboni.

Adakana kulakwa: Banda ndi mkazi wake akuyankha mlandu  wosapereka chisamaliro kwa ana awo
Adakana kulakwa: Banda ndi mkazi wake akuyankha mlandu
wosapereka chisamaliro kwa ana awo

Sabata yatha, apolisi ya Manase mumzinda wa Blantyre adanjata Peterson Mtchini Banda, wa zaka 44, ndi mkazi wake Agnes, wa zaka 41, atatsinidwa khuku kuti banjali silimatuluka m’nyumba kuyambira m’chaka cha 2013.

Mneneri wa polisi ya Blantyre, Elizabeth Divala, wauza Msangulutso kuti banjali lidauza apolisiwo kuti adachita izi ngati njira imodzi yodzitetezera kwa anthu achipongwe.

“Akuti tsiku lina bamboyo adafuna kuchitidwa chipongwe ndi anthu ndipo nkhaniyo ati adafotokozera apolisi koma sadaione mutu wake. Kuyambira panthawiyo, iye akuti adauza banja lake kuti asadzatulukenso m’nyumbamo,” adatero Divala.

“Moti tsiku lomwe tidapita kunyumbako, tidagogoda koma sadatsegule, tidagwiritsira ntchito mphamvu pothyola chitseko ndipo tidawapeza makolowo komanso ana awo anayi akuoneka ofooka. Tidawatengera kupolisi kuti tidzawafunse.”

Banjali akuti lidauza apolisiwo kuti akafuna ndiwo, kapena chakudya chilichonse, amaitana anthu amene ayandikana nawo ndi kuwapatsira ndalama kuti akawagulire zomwe akufunazo.

“Nyumbayo ili kumpanda, ndiye chilichonse chili kumpandako monga chimbudzi komanso madzi. Ali ndi nyumba za lendi zomwe amatolera ndalama pakutha pa mwezi, ndalama amazipeza motero ndipo ati amadzawapatsira ndalamazo pazenera,” adatero Divala.

Chidzitsekerereni m’nyumbamo mu 2013, ana a banjali akuti adawaleketsa sukulu. Pano mwana woyamba ndi wa zaka 17, wina 14, wina 11 ndi wina wa zaka zinayi.

Divala wati makolowo adawatsegulira mlandu wolephera kupereka chithandizo kwa ana awo.

“Anawo adawaleketsa sukulu, komanso matupi awo amaoneka ofooka chifukwa chosowa zakudya zomwe ndi zotsutsana ndi gawo 165 la malamulo a dziko lino,” adatero Divala. n

Related Articles

Back to top button