Chichewa

Obzala nthawi ya maliro athothedwa

Thambo likagwa m’mudzi, aliyense amayenera ayandikire chifupi ndi siwa kuti athandizane nthawi ya zolemetsayi. Kudagwa zovuta m’mudzi mwa Mazale kwa Senior Chief Kapeni m’boma la Blantyre. Nthawi yokagoneka mfumu itakwana, ena ndiye adali kalikiriki kubzala. Izi zidakwiyitsa adzukulu. Ndiyetu kudali kuwathamangitsa. BOBBY KABANGO adali nawo komweko ndipo adacheza ndi mfumu Mazale pa za anthu ophwanya mwambowa motere:

Ulendo wa kumanada: Aliyense akuyenera kupezekako
Ulendo wa kumanada: Aliyense akuyenera kupezekako

Pepanitu mfumu…

Aaa lekani wawa.

Choyamba tatifotokozereni za zovutazi…

M’mudzi muno tidali ndi kamnyamata kena kamene kadali msangulutso wa aliyense, kochezeka komanso kakhalidwe labwino. Kanangodwala katapita ku Bangwe kwa makolo ake. Kukatengera kuchipatala basi ndagona pano. Mnyamata ameneyu adali Manuel German.

Pepani ndithu, paulendo paja tidaona anthu akuthamangitsana, chidachitika n’chiyani?

Sindidziwa kuti ndinu amtundu wanji, koma kwathu kuno, maliro akachitika, timayenera tonse tilire limodzi. Zilibe kanthu kuti watangwanika komabe timayenera tisonkhane chifukwa izi ndi zadzidzidzi, palibe amene amafuna kuti zitero. Ndiye chidachitika apa n’chakuti pamene timati tinyamuke kuperekeza mfumu yathu, basitu tidangodabwa kuona anthu ena akubzala mbewu zawo m’minda.

Ndiye adzukulu adawalondola kuti amve vuto lawo lidali chiyani.

Adangowalondola? Ndaonatu akuwathamangitsa…

Eya ndiye kuwalondolako. Kudali kumva za vuto lawo kuti azibzala pamene tonse tikulira. Adawalonda mpaka adataya mbewu koma cholinga kudali kuwatenga. Mwamvanso adzukulu akudandaula kumanda kuja, zimenezo ndi zolakwika kumagwira ntchito pamene anzako akulira.

Kodi n’kulakwa kugwira ntchito pamene ena ali pachisoni?

Kwambiri, masiku ano mwambo wathu sukutsatidwanso. Umenewu ndi mlandu ndithu ndipo siziyenera zizitero. Ngati m’mudzi wina mwachitika zovuta, timayenera midzi yonse yoyandikana tilire pamodzi.

Ngati wasemphana ndi izi ndiye zimatani?

Ndi mlandu, mwawamva adzukulu akuti zikachitikanso adzamugwira munthuyo ndi kumumangirira kumanda komanso kumukumbitsa dzenje komanso akwirire yekha. Koma amene amabzala lerowa ndiye ndawauza amfumu awo kuti awaitanitse ndipo agwe ndi mbuzi kapena nkhuku. Uku ndi kunyoza kwambiri, kodi iwowo samwalira?

Related Articles

Back to top button