Chichewa

Odzipha akuchuluka

M’chaka cha 2020 chiwerengero cha anthu odzipha chidakwera poyerekeza ndi cha m’chaka cha 2019.

Kafukufuku wa apolisi akuonetsa ku chiwerengerochi chidachoka pa 166 miyezi ya January mpaka August chaka cha 2019 kukafika pa 182 miyezi ngati yomweyi m’chaka cha 2020.

Wachiwiri kwa mneneri wa apolisi m’dziko muno, Peter Kalaya, ndiye adapereka chiwerengerochi.

Iye adati ambiri mwa anthuwa adali amuna a zaka zapakati pa 15 ndi 40.

An illustration of court proceedings

Kalaya adati ambiri amadzipha kaamba ka mavuto a za m’banja, komanso nkhani zachuma.

Iye adati apolisi akupepha Amalawi kuti akakumana ndi mavuto azipita ku victim support unit yomwe ali nayo pafupi kukalandira uphungu.

“Kudzipha si yankho chifukwa pali njira zina zabwino zothesera mavuto,” adatero mkuluyu.

Ngale Massa, katswiri wa za kaganizidwe ka munthu, adapempha anthu kuti afunsa uphungu kwa anzawo akakumana ndi mavuto.

Malingana ndi zotsatira zakafukufuku yemwe bungwe la St John of God lidatulutsa mwezi wa November 2020, mwa anthu 100 aliwonse omwe amadzipha 80 ndi amakhala abambo.

Kafukufukuyu akusonyeza kuti 57 mwa 100 anthu aliwonse adadzipha podzimangirira pamene 30 mwa 100 aliwonse adagwiritsa ntchito chiphe.

Kafukufukuyu akuti mchitidwewu ukuchuluka chifukwa chosowa ukadaulo pa kaganizidwe koyenera.

Katswiri wina pa nkhani ya kaganizidwe wa pa sukulu ya College of Medicine, Chiwoza Bandawe, adati n’zokhumudwitsa kuti chiwerengero cha ana odzipha chikukweranso.

“Anthu ambiri safuna kufa, koma kuchotsa ululu womwe akukomana nawo.

“Amaganiza kuti akadzipha ndiye kuti athana ndi mavuto omwe akukumana nawo,” adatero Chiwoza.

Iye adati chiwerengero cha anthu odzipha chitha kutsika Amalawi ambiri ataphunzira kaganizidwe koyenera, komanso njira zothetsera mavuto awo.

Related Articles

Back to top button