Chichewa

Okakamira milongoti zawo izo!

Listen to this article

Lachitatu likubwelali lidzakhala tsiku lowawa kwa iwo amaonera kanema ya mlongoti (aerial).

Makanema ambiri adzazima ndipo kudzakhala mdima wadzaoneni. Patsikulo ena adzayesa kuzimitsa makanema awo n’kuyatsanso koma sadzayaka ndipo ena adzawatengera kwa okonzetsa koma chithunzi osaoneka. Koma awa si mathero a dziko.

Okhawo omwe ali ndi zowayenereza kuonera kanema wawo munjira yatsopano ya dijito adzaona kuwala. Awa ndi mathero a zithunzi zamchengamchenga ndinso zooneka ngati mvula ikuwaza pakanema.

M’chaka cha 2006 bungwe la United Nations (UN) lidagwirizana kuti maiko onse asiye kugwiritsa ntchito zithunzi zamchengamchenga n’kupita kudijito.

Bungweli lidati ndi dijito zithunzi za kanema zizioneka zopanda mchengamchega komanso mawu azimveka bwino opanda manzenene.

Koma kodi ndi angati akudziwa za kusinthaku? Mwa anthu khumi omwe tidawapeza m’mzinda wa Mzuzu, atatu ndi amene akudziwa za kusinthaku.

A bungwe loona za ogula la Consumers Association of Malawi (Cama) ati boma lilibe nazo ntchito kwenikweni za kusinthaku.

“Ndi zoonetseratu kuti boma silikukhudzidwa ndi kusinthaku chifukwa silikudziwa chomwe likuchita, ndi anthu omwe silidawadziwitse mokwanira za kusinthaku,” adatero John Kapito, mkulu wa bungweli.

Nayo nduna ya zofalitsa nkhani, Kondwani Nankhumwa, mmbuyomu idavomereza kuti boma lalephera kudziwitsa anthu mokwanira za kusinthaku.

Koma mkulu wa bungwe loyang’anira za kusinthaku la Malawi Digital Broadcasting Network Limited (MDBNL), Dennis Chirwa, adati bungwe lake layesetsa kuchita zomwe lingathe.

Iye adati bungwe lake lagula ma decoder omwe akugulitsidwa m’mapositi ofesi onse m’dziko muno pamtengo wa K20 000.

Related Articles

Back to top button