Nkhani

Okhala kumalire ku Phalombe akulira

Listen to this article
Ena mwa amayi adafika kumsonkhanowo
Ena mwa amayi adafika kumsonkhanowo

Anthu ena ku Phalombe adandaula ndi nkhanza zimene amachitiridwa akapita m’dziko la Mozambique ndiponso ndi chiwerengero cha ana obedwa m’bomalo.

Mchitidwe woba ndi kuzembetsa ana wanyanya ndipo ku Phalombe zankitsa chifukwa chaka chino chokha ana 14 abedwa kale, pomwe chaka chatha ana asanu ndiwo adasowetsedwa.

Izi ndi malinga ndi lipoti la polisi m’bomalo lomwenso lasonyeza kuti ku Zomba ana anayi okha ndiwo abedwa pomwe Maboma a Mangochi, Machinga, Chiradzulu ndi Mulanje palibe amene wasowetsedwa.

Anawatu ndi a zaka zosaposa 18 ndipo ambiri akumanamizidwa kuti akukawalemba ntchito koma akafika m’dzikolo akumagwiritsidwa ntchito yogulitsa matupi awo kapena kugwira ntchito zosalingana ndi misinkhu yawo.

Si kusowetsedwa kwa ana kokha komwe kwanyanya m’boma la Phalombe, nzika za dziko lino akuti zikalowa ku Mozambique zikumalipitsidwa kapena kumenyedwa pamene nzika za ku Mozambique zikalowa m’dziko muno savutitsidwa.

Nawo achitetezo a m’dziko la Mozambique akuti akumalowa m’dziko muno ndi mfuti pomwe ena atavala zovala zapolisi.

Izi zidachititsa kuti anthu a magulupu a Chinani, Nthambula, Nambazo, Mpinda komanso Mtemanyama kwa T/A Nazombe ndi Senior Chief Chiwalo asonkhane pamsika wa Mphwisi kuti apereke madandaulo kwa mkulu wa apolisi kuchigawo chakummwera.

Gogo Lone Tawanga wa m’mudzi mwa Chinani adati chifukwa cha njala amapita ku Mozambique komwe amakalimitsa chinangwa kuti adzadye ndi ana ake koma chaka chatha atapitako adagwidwa ndi asilikali a m’dzikolo.

“Adandimenya ndipo adati ndilipire K1 500 ngati ndikufuna ndidzipulumutse. Nditanenerera ndidapereka K600. Timadabwa kuti tikalowa m’dziko lawo timazunzidwa koma iwo amalowa m’dziko muno popanda vuto,” adadandaula Tawanga.

Nyakwawa Mandawala ya mwa Senior Chief Chiwalo idati nayonso idagwidwa pamene imakagula ufa wophikira mandasi ndipo idalipitsidwa. Koma kudabwa kwa mfumuyi ndikoti zikutheka bwanji anthu a m’dziko la Mozambique savutitsidwa akalowa m’dziko muno.

“Tikudabwa kwambiri, chifukwa chiyani boma lathu likulekerera kuti tizizunzidwa motere? Ana athu akutengedwa nthawi iliyonse,” idatero mfumuyo yomwe idalankhula mokwiya kwambiri.

Mandawala adaonjeza kuti ndi bwino boma likhwimitse chitetezo kuti anthu a m’dzikolo asamangolowa m’dziko muno mwa chisawawa ndipo akagwidwa azilangidwa, ganizo lomwe lidavomerezedwa mokweza mawu ndi anthu oposa 300 amene adasonkhana panthawiyo.

Nkhumano omwe udalipo Lachiwiri m’sabatayi udakonzedwa ndi bungwe la mpingo wa Katolika loona za chitukuko la Catholic Development Commission (Cadecom) ndi thandizo lochokera ku Caritas Austraria. Bungweli lidakhazikitsa magulu omvera wailesi m’bomali amene amathandiza kuulutsa nkhani zomwe zimachitika m’midzi.

Peter Pangani wa bungwe la Cadecom adati kaamba ka mavuto amene anthu akhala akukumana nawo m’bomali nchifukwa chake adapanga nkhumanowo kuti adindo ndi mafumu adzimvere mavuto amene anthu m’bomalo akukumananawo.

“Tidapempha a bungwe la Develpment Communications Trust (DCT) amene ndi akadaulo pa zofalitsa nkhani kuti agwire ntchito ndi amagulu omvera wailesiyi kuti tikhale ndi tsiku lomwe anthu angapereke nkhawa zawo. Ife tasangalala kuti adindo adzimvera okha za mavuto amene akukumana nawo ndipo mayankho eya ayamba kale kuperekedwa,” adatero Pangani.

Koma mkulu wa apolisi kuchigawo chakummwera, Wilson Matinga adatsimikizira anthuwa kuti pakhala kusintha. Iye adati chitetezo sichingakhale ngati apolisi alipo ochepa komanso ngati palibe galimoto zoyendera. Polisi ya Phalombe ili ndi galimoto imodzi yomwe siifikira m’madera onse.

“Tamva anthu alankhula, ndipo akunena zoona. Koma tikuwatsimikizira kuti pakhala kusintha, ndikamba ndi anzanga a dziko la Mozambique kuti mavutowa athe.

“Wapolisi wa dziko lawo saloledwa kulowa m’dziko muno atavala zachitetezo kapena kunyamula mfuti. Tikutumizanso asilikali ena kuti mwina akwane 7 ndi amene alipo kale kudera lino cholinga chitetezo chikhwime,” adatero Matinga.

DC wa bomalo Paul Kalilombe adauza apolisi kuti akatenge njinga yamoto kuofesi kwake kuti ithandize apolisi kukhwimitsa chitetezocho. Naye Senior Chief Chiwalo adagwirizana kwathunthu ndi zomwe anthu ake adadandaulira akuluakuluwa.

Njira yaulere yomwe anthu amaimbira foni mwa ulere kupereka madandaulo awo ya Child Help Line 828 (CHL 828) ikuwonetsa kuti pofika mmwezi wa June chaka chino, ana 684 ndiwo adataidwa, ana 14 adabedwa, 195 ndiwo amagwiritsidwa ntchito zoposa msinkhu wawo, 53 ndiwo adakakamizidwa kukalowa banja, 259 ndiwo adachitidwa nkhaza monga kumenyedwa komanso ana 25 amene adagwiriridwa m’dziko muno.

Related Articles

Back to top button
Translate »