Nkhani

Olowa m’dziko mozemba aonjeza mavuto m’ndende

Listen to this article

Mavuto a m’ndende za m’dziko muno ngosakamba koma kafukufuku wa Tamvani wasonyeza kuti ena mwa mavutowa akudza kaamba ka anthu osamangidwa koma ongosungidwa m’ndende chifukwa cholowa m’dziko muno popanda chilolezo.

Malingana ndi wachiwiri wa mneneri wa nthambi yoona za anthu olowa ndi kutuluka m’dziko muno, Wellington Chiponde, chiwerengero cha anthu oterewa chimasinthasintha kaamba koti yemwe wakonzeka amatuluka n’kumanka kwawo.

Ena mwa olowa m’dziko muno popanda chilolezo atawagwira ku Nkhata Bay
Ena mwa olowa m’dziko muno popanda chilolezo atawagwira ku Nkhata Bay

“Aliyense mwa anthuwa amadzionera yekha chochita kuti abwerere kwawo, chifukwa boma siliperekapo chilichonse kupatula kuwadyetsa ndi kuwasunga pamalo okhazikika, omwe n’kundendeko,” adatero Chiponde.

Iye adati anthuwa sakhala kundendeko ngati akayidi koma ngati njira yowathandizira malo okhala ndi chakudya poyembekezera kuti azipita kwawo akakonzeka polingalira kuti dziko lino lilibe malo osungirako nzika za maiko ena zolowa m’dziko muno popanda chilolezo.

Chiponde adati malamulo amalola anthu oterewa kusungidwa m’ndende kwa sabata ziwiri zokha ndipo ikakwana nthawiyi amafunsidwa ngati apeza njira yopitira kwawo, koma ngati njirayo sidapezeke, amawapatsanso masiku ena kufikira pomwe adzakonzeke kubwerera kwawo.

“Si nkhanza, ayi, koma malamulo a dziko amatero kuti nzika ya dziko lina si yoyenera kukhala m’dziko muno popanda chilolezo pazifukwa zingapo. Mudziwa kuti boma limayenera kupanga ndondomeko ya zinthu zambiri monga chitetezo, mankhwala, chakudya ndi zina.

“Kuti ndondomeko imeneyi iyende bwino, boma limayenera kudziwa chiwerengero cha anthu omwe ali m’dziko nchifukwa chake othawa nkhondo kapena odzausa mwandondomeko amakhala ndi zowayenereza ndipo amakhala ndi malo awoawo,” adatero Chiponde.

Iye adati malamulo oterewa ali m’dziko lililonse ndipo maiko ena ali ndi malo akeake osungirako anthu oterewa koma poti dziko lino likadalibe malowa, limasunga anthuwa m’ndende.

Potsirapo ndemanga pankhaniyi, mneneri wa zandende m’dziko muno, Smart Maliro, adati ichi n’chipsinjo chachikulu kwa akuluakulu oyang’anira za ndende polingalira kuti iwo amayenera kuti azidyetsa ndi kuyang’anira anthuwa kufikira pomwe adzatuluke.

Naye adati chiwerengero cha anthuwa chimasinthasintha kutengera ndi momwe akulowera komanso kutuluka koma zonse zimatengera kuti a nthambi yoona za anthu olowa n’kutuluka anenanji.

“Ife timangolandira n’kusunga anthuwa koma zonse amayendetsa ndi anthambi yoona za anthu olowa n’kutuluka m’dziko chifukwa sikuti anthuwa ndi omangidwa, ayi. Nkhawa yathu imangokhala pachisamaliro chifukwa zonse zimagwera ife.

“Mwachitsanzo timayenera kupeza malo oti akhalepo, chakudya komanso poti chiwerengero cha anthu m’ndende chimakwera, zinthu monga madzi ndi zina zimagwira ntchito kwambiri ndiye mabilu nawo amakwera,” adatero Maliro.

Nawo oyang’anira za maufulu a anthu ati zomwe amaona anthu olowa m’dziko mwachinyengowa n’zopweteka komanso zowaphwanyira ufulu kaamba koti amasungidwa m’malo oyenera omangidwa.

Mkulu wa bungwe la Centre for Human Right and Rehabilitation (CHRR), Timothy Mtambo, adati ndende za m’dziko muno zili ndi mbiri zosakhala bwino, makamaka pankhani yothithikana, zaumoyo ndi kuvuta kwa chakudya.

Mkuluyu adaona kuti kusunga anthuwa m’malo ngati amenewa n’kuwalakwira kwambiri potengera malamulo a zaufulu wa anthu padziko lonse.

“Kumeneko n’kulakwa chifukwa anthuwa sadamangidwe, ayi, akungoyenera kutumizidwa kwawo basi osati mpaka kumasungidwa m’ndende ngati kuti azengedwa mlandu n’kumangidwa,” adatero Mtambo.

Iye adati njira yabwino n’kumanga malo osungirako anthu oterewa poyembekeza kuti azinka kwawo monga momwe zilili m’maiko ena.

Nduna ya zam’dziko, Jappie Mhango, adati ganizo lomanga malo osungilako anthuwa ndi labwino, makamaka pankhani yachitetezo, koma adati pakalipano palibe mapulani otere polingalira mavuto a zachuma omwe ali m’dziko muno.

“Ndi maganizo abwino kwambiri chifukwa anthuwa amachokera kosiyanasiyana ndiye sitinganeneretu kuti moyo wawo ndi wotani. Mwina ena adali zigawenga zikuluzikulu kwawo, akhoza kuphunzitsa anthu anthu omwe ali m’ndende,” adatero Mhango.

Iye adati mtsogolo muno zinthu zikadzayamba kuyenda bwino, boma lidzaganizirapo kuti mwina lidzamange malo osungirako anthuwa kuti azikakhala kwaokha.

Related Articles

Back to top button