Chichewa

One-man demo pa Wenela

 

tsikulo pa wenela padaterera. zidaliko. nkhani idavuta ndi ija tidaiyamba sabata yatha. Inde, iyi nkhani yophana chisawawa, makamaka kwa abale athu achialubino.

Izi zikumvekazi zidandikumbutsa zomwe ndidamvapo mmbuyomu kuti Manyasa kalelo ankaponyera kuphompho odwala khate, kuja ku Zomba. Mitembo yawo inkapezeka mumtsinje wa Namitambo. Koma nanga lero zoona kuphanaku zatani?

Abiti Patuma adali pafoni ndipo amangodzuma. Uku tidali tikuonera kanema.

“Zoona pa CNN, BBC, Al Jazeera ndi ena onse akunja akufalitsa za nkhanza tikuchitirana tokhatokhazi! Kodi izi ndiye azungu abweranso kuno kwathu kudzatisiyira enafe ma dollars, ma rands ndi zina zotero?” adafunsa.

art

“Zonsezi ndi Moya Pete ndi anzake. Izitu sizikadafika apa akadalimbana nazo koyambirira komwe kuja. Nkhani zikangokhudza United Nations komanso Amnesty International umangodziwiratu! Mwaiwala adathana ndi gogo uja ndani?” adatero Gervazzio.

Zoona, ndikumbuka masiku amenewo ndili kwathu kwa Kanduku, tinkamva kuti bungwe la Amnesty International lidalimbikitsa kuti zinthu kuno zisinthe makamakanso chifukwa cha kumangidwa kwa andale ena popanda chifukwa komanso kuphedwa kumene.

“Mwaiwalanso muja UN idavutira nthawi ya Mfumu Mose? Zoti munthu ngwamakani kuiwaliratu,” adatero Abiti Patuma.

“Chomwe ndikudabwa ine nchakuti dziko lino lidaliko kuyambira kale koma izi zachuluka chomwechi nthawi ya Moya Pete, bwanji?” ndidafunsa.

Palibe adandiyankha. Adangoti duuu!

Posakhalitsa adatulukira mkulu wina ali chibadwire. Iyetu adanyamula chikwangwani cholemba kuti ‘Osapha!’ Tonse tidayang’ana kumbali.

Abiti Patuma adathawira kukauntala, adatenga chikwama chake pomwe amasungitsapo nkusololamo chovala chamkati chofiira.

“Chonde, atate, amamangatu izi zoyenda bunobunozi. Amene samangidwa ngwamisala basi. Tavalani basi, tilibetu ndalama zogulira nthochi kuti tizikakuonani akakunjatani,” adatero Abiti Patuma.

Kaya mkulu uyu ndidamuonapo kuti kaya? Koma nkhope yake ndi yosasowa.

“Ndipo tangoganizani kuyenda malipsata mukuchitako, Paparazzi akatola zithunzi nkuika munyuzi, mwana wanu nkuona, ulemu wanu ukhalaponso?” adatero Gervazzio.

Nkhope yakeyo si yosowa, koma kaya ndidamuona kuti mkulu ameneyu? Kodi ndi uja adali ndi bwenzi lonenepa zedi ankalimbirana ndi mnyamata wa magitala uja?

“Tonse takwiya, koma chonde ife zomationetsa filimu zolaula masanasana takana. Akapanda kukutenga apolisi tiitanitsa a Censorship Board,” adatero Abiti Patuma.

“Mwamaliza? Ndakwiyatu kwambiri. Ndine legistrator, ntchito yanga ndi yopanga malamulo. Apapatu aphungu komanso boma timayenera kubweretsa Group Areas Act chifukwa nkhaniyi ikuposa nkhani ya njala,” adatero mkulu uja, thovu likukha.

“Dekhani, achimwene. Anzanu enatu adayamba ndi matukutuku chomwechi koma adakathera kuti atapezeka kuti satifiketi ya 8 adalibe?” adafunsa Abiti Patuma.

Kaya mkulu ameneyu ndidamuonapo kuti? Koma atavala bulauzi ndi phwanyamchenga zingamukhale bwanji!

“Kaya mundipha, kaya mundidya, ine ndivula basi,” adafuna kuchotsa kabudula wamkati adapatsidwa ndi Abiti Patuma uja.

Ndamukumbukira mkulu uyu. Suja ankati azungu oteteza nkhalango ya Mulanje akapanda kupita kwawo iyeyo awalodza basi?

Gwira bango, upita ndi madzi usanavale! n

 

Related Articles

Back to top button