Chichewa

OPEZEKA KUMANDA AYANKHA MLANDU

Listen to this article

 

Anthu a m’mudzi mwa Yesaya Nkosi Mfumu kwa Inkosi Chindi m’boma la Mzimba adadzidzimuka ataona galimoto yachilendo itaimitsidwa pamanda a m’mudzimo pomwe anthu anayi adali kuchita chizimba kumandako.

Mneneri wa polisi m’boma la Mzimba, Gabriel Chiona, adatsimikiza za nkhaniyi ponena kuti iwo adanjata anthu anayi omwe akuganiziridwa mlandu wokhala pamalo popanda chilolezo ndipo iwo adakaonekera kubwalo la milandu la majisitireti Lachinayi pa 20 August.
court
Chiona adati anthuwo ndi Koloboyi Mwazembe, wa zaka 35, wochokera m’boma la Chitipa; Esau Simwimba, wazaka 36, wochokeranso ku Chitipa; Tenson Mhone, wa zaka 65; ndi Chrissy Phiri, wa zaka 73, onse a m’boma la Mzimba.

Malinga ndi Chiona, Mwazembe ndi Simwimba alamulidwa kukakhala kundende kwa chaka chimodzi kapena apereke chindapusa cha K90 000 atawapeza olakwa pamlandu wopezeka kumanda popanda chilolezo.

Koma Phiri ndi Mhone adzalowanso m’bwaloli sabata ino kuti adzayankhe milandu yopezeka pamalo popanda chilolezo komanso kuba mwachinyengo, milandu yomwe iwo aikana.

Chiona adati anthuwo adanjatidwa pa 13 August pomwe mfumu Msipani Nyirenda adauza apolisi za anthu omwe adali kumanda a m’mudzimo.

Malinga ndi Chiona, bambo wina adaona galimo ya oganiziridwawo itaima kwa nthawi yaitali pafupi ndi manda a m’mudzimo, zomwe zidamuchititsa kuti akanene za nkhaniyi kwa nyakwawa yemwe adatsina khutu apolisi.

“Anthu a m’mudzimo adawagwira oganiziridwawo panthawi yomwe amatuluka kumanda. Mmodzi mwa oganiziridwawo adanyamula chithumwa, komanso adapezeka ndi ndalama zokwana K700 000,” adatero Chiona.

Msangulutso utafunsa mmodzi mwa oganiziridwawa, Phiri, kuti afokotokoze zomwe ankachitika kumandako, iye adati amafuna chizimba cha bizinesi ndipo chithumwa chomwe adali nacho n’chokawira anthu ndalama.

“Chithumwachi chimakawa anthu ndalama. Muli njoka yomwe imakhala ikukawa anthuwa ndalamazo,” adatero Phiri.

Phiri adati bambo wina adagula njoka kwa sing’anga, Mhone, yomwe imakawa anthu ndalama koma njokayo idathawa. Iye adati njokayo itathawa iye adaganiza zokagula ina yomwe sing’angayo adati idali kumanda komwe adapezekako.

Khansala wa derali, Dan Nkosi, adathirira ndemanga za nkhaniyi ponena kuti apolisi adabwera kunyumba kwakwe kudzamutenga kuti akaone zomwe zidachitikazo.

“Ndidapeza anthu atawagwira oganiziridwawo kupita nawo kwa mfumu Msipani Nyirenda komwe adafunsidwa zomwe amachita. Iwo adafotokoza kuti amagulitsana chizimba pamtengo wa K700 000 chomwe tidawapeza nacho,” adatero Nkosi kuuza Msangulutso.

Mfumu Msipani Nyirenda sadathe kupezeka kuti ayankhulepo pankhaniyi.

Related Articles

Back to top button