Chichewa

Osabweza ngongole ya Mardef ali m’madzi

 

Anthu amene sadabweze ngongole ya Malawi Enterprise Development Fund (Mardef) ali m’madzi pamene ayamba kuona zakuda.

Ngongole ya Mardef idayamba nthawi ya ulamuliro wa Bingu wa Mutharika pomwe amapereka ndalama kwa achinyamata kuti ayambire bizinesi. Koma ambiri mwa anthuwo sanabweze ngongoleyo.

Malinga ndi anthu ena amene tacheza nawo m’boma la Kasungu, anthu amene sadabweze ngongoleyi ayamba kumangidwa pamene ena akuwalanda katundu.

Mneneri wa Mardef Isaac Mbekeani watsimikiza kuti bungwe lawo layamba kutoleradi ngongoleyo m’boma la Kasungu ndi maboma ena. Koma iye adati timupatse mpata kuti afufuze kuchuluka kwa anthu amene akuwafufuza ngakhalenso ndalama zimene zikufu nika.

loan

“Tumizireni mafunso ndipo ndikuyankhani tsatanetsatane wake za nkhaniyi,” adatero Mbekeani Lachinayi koma pofika Lachisanu n’kuti asadayankhe mafunsowo.

Koma nyakwawa Alamu ya pamsika wa Nkhamenya adatsimikizira Msangulutso kuti anthu ena anjatidwa koma sadapereke zambiri pankhaniyi.

“M’mudzi mwanga mulibe amene ali ndi ngongoleyi chifukwa iwo amene adakongola nawo adabweza kale ngongoleyo, koma madera ena m’boma lino ndiye anthu ali pakalapakala,” idatero mfumuyo.

Mayi ena amene sadafune kutchulidwa koma akukhala pamsika wa Nkhamenya m’bomalo, adati anthu amene sadabweze ngongoleyi ayamba kubisala.

“Pamene zidamveka mwezi watha kuti amene sadabweze ngongoleyi ayamba kuwamangitsa, anthu ena asamuka kuno pamene ena akumabwera usiku wokhawokha ndi ena athawiratu.

“Ngati sudabweze ngongoleyi akumakumangitsa, apo ayi ena akumawatengera zinthu monga mwa mgwirizano wa ngongoleyo,” adatero. amene adakongola nawo adabweza kale ngongoleyo, koma madera ena m’boma lino ndiye anthu ali pakalapakala,” idatero mfumuyo.

Mayi ena amene sadafune kutchulidwa koma akukhala pamsika wa Nkhamenya m’bomalo, adati anthu amene sadabweze ngongoleyi ayamba kubisala.

“Pamene zidamveka mwezi watha kuti amene sadabweze ngongoleyi ayamba kuwamangitsa, anthu ena asamuka kuno pamene ena akumabwera usiku wokhawokha ndi ena athawiratu.

“Ngati sudabweze ngongoleyi akumakumangitsa, apo ayi ena akumawatengera zinthu monga mwa mgwirizano wa ngongoleyo,” adatero. n

Related Articles

Back to top button