Chill

Osagulitsa chakudya—Unduna

Listen to this article

 

Kunjaku mitengo ya chakudya makamaka chimanga yafika pokhetsa dovu koma unduna wa zamalimidwe, ulimi wothirira ndi chitukuko cha madzi wati anthu asakopeke ndi mitengoyi nkuyamba kugulitsa chakudya chomwe ali nacho.

Woyang’anira ntchito zaulangizi wa njira zamalimidwe amakono muundunawu Stella Kamkwamba adati anthu asamale kwambiri chakudya chawo kuopa kuti angadzawone zakuda atagulitsa nkuyamba kuvutika ndi njala.

Alimi sayenera kugulitsa chimanga chonse kuli njala
Alimi sayenera kugulitsa chimanga chonse kuli njala

Selling-maize

“Anthu asamale chakudya chawo osagulitsa kapena kudya mowononga chifukwa sizikudziwika kuti mvula igwa bwanji chaka chino monga mmene yayambira kalemu kuduladula,” adatero Kamwamba.

M’madera ambiri, mtengo wa chimanga wakwera ndi kawiri kapena katatu kuposa mtengo wa kumsika wa Admarc omwe umagulitsa chimanga ndi mbewu zina m’malo mwa boma kuti anthu azigula pamtengo otsika.

Malingana ndi dandaulo lakuti chimanga chikusowa m’misika yambiri ya Admarc, mavenda adasokolotsa chimanga chawo nkuyamba kugulitsa pamtengo wokwera.

Kafukufuku wa nyuzipepala ya The Nation adasonyeza kuti mtengo wa chimanga mumzinda wa Blantyre uli pa K10 000, K9 600 ku Mzuzu ndipo K9 500 ku Zomba ndi K9, 000 mumzinda wa Lilongwe thumba la makilogalamu 50.

Mitengoyi ikukwererakwererabe zomwe zikuopsa chifukwa anthu akhoza kukopeka nkuyamba kugulitsa chomwe adasunga kuti azidya poika mtima pa ndalama.

“Mitengo yake imeneyi, ukhoza kupezekadi kuti wakomedwa nkugulitsa chomwe udasungira patsogolo moti anthu alingalire bwino zomwe akunena a undunawu apo ayi wina adzalira ching’ang’adza ndithu,” adatero William Kalimba wa mumzinda wa Lilongwe.

Kamkwamba adati nyengo yomwe tikulowayi chimanga cha m’madimba chomwe ena adabzala chimakhala chikucha ndipo kumakhala pikitipikiti kugulitsa mondokwa mpaka dimba lonse kutha mmalo mosiyako china kuti chiwume.

“Nthawi zambiri, nyengo yoti mbewu zacha, kumakhala zodabwitsa kuona mmene anthu akusakazira, kuyiwala pa mawa moti alimi omwe mbewu zawo zikucha m’madimba asamale kwambiri,” adatero Kamkwamba

Related Articles

Check Also
Close
Back to top button