Chichewa

Osangoti neba akuweta nkhumba

Atangomva kuti ulimi wa nkhumba ndi waphindu Leckner Kanyama wa m’boma la Lilongwe adayamba ulimiwu mwansangala poganiza kuti atola chikwama.

Mlimiyu adayamba ndi nkhumba 4; yaimuna imodzi ndi zazikazi zitatu.

Posakhalitsa, nkhumba zazikazizo zidatenga bele ndipo iliyonse idaswa ana osachepera 10.

“Apa ndidajowa ndi chisangalalo chifukwa ndalama zija ndidayamba kuziona koma zomvetsa chisoni tiana tija tambiri tidatha ndi kufa.

“Chigodola nacho chidabuka m’dera lathu ndipo khola langa silidasemphedwe,” adadandaula motero mlimiyo.

Alimi amene amakonzekera bwino ulimiwu amapha makwacha a nkhaninkhani

Padakalipano Kanyama akuti akunka nafufuza upangiri pa mmene angasamalirire tiana ta nkhumba komanso kuthana ndi matenda a chigodola.

Mlimiyu ndi mmodzi mwa alimi a nkhumba m’dziko muno amene mmalo mopindula ndi ulimiwu amangolowetsa ndalama zawo pa chabe ndipo ena adagwa mphwayi saukhumbira n’komwe.

Mphunzitsi wa zaulimi wa ziweto ku Lilongwe University of Agriculture and Natural Resources (Luanar) Jonathan Tanganyika akuti alimi ambiri m’dziko muno ulimiwu umawakanika chifukwa chosakonzekera mokwanira.

“Kusowekera upangiri kumbali ya mbewu yabwino, mmene angamangire khola ndi mpanda wothandiza kuti zitetezeke ku chigodola, mmene angatetezere pamalopo kuti pasafike matendawa kumawaika alimi ambiri pamavuto.

“Kusakonzekera mokwanira zipangizo ndi upangiri wa kapangidwe ka chakudya cha kasakaniza, kusapereka mchere wa iron kwa ana a nkhumba akangobadwa pasanathe masiku atatu ndi kusalumikizana ndi alangizi pafupipafupi mlimi akayamba kuweta zimalowetsa pansi ulimiwu,” iye adatero.

Kadaulo wa ziweto m’boma la Kasungu Jacob Mwasinga adaonjeza kuti nkhumba zimafunika kuzimwetsa mankhwala opha nyongolotsi za m’mimba m’miyezi itatu iliyonse.

“Mlimi akapanda kutero zimanyentchera choncho sangapeze phindu. Kusakonzekera chakudya chokwanira chaka chonse nako kumanyentcheretsa nkhumba chakudya chikasowa,” iye adatero.

Malingana ndi mkulu wa Shire Valley Agriculture Development Division (Shvadd) Francis Mlewah yemwenso ndi kadaulo wa ziweto adati tiana ta ziweto monga nkhumba pafupifupi 30 pa 100 tilitonse timafa kaamba ka njoka za m’mimba.

Iye adafotokoza kuti njoka za m’mimba ndi zoopsa chifukwa zimayamwa chakudya ndipo izi zikachitika kwa kanthawi chiweto chimafa mosavuta.

“Chikakhala chigodola alimi akumbukire kuti chikalowa m’khola chimasesa nkhumba zonse choncho akuyenera kuvala zilimbe,” iye adatero.

Tanganyika adathirirapo ndemanga kuti tiana tankhumba timafa m’sabata zinayi kuchokera pamene zaswedwa kaamba kosapatsidwa mchere wa iron.

Iye adafotokoza kuti izi zili chomwechi chifukwa mkaka wa mayi wawo umakhala ndi mcherewu ochepa chabe choncho umatha m’sabata zitatu zokha.

Zotsatira zake mphunzitsiyu adati tiana tambiri timafa chifukwa cha kusowa kwa magazi m’thupi.

“Ichi n’chifukwa chake mlimi afune kapena asafune akuyenera kupatsira mcherewu pasadathe masiku atatu chifukwa kupanda kutero sizikhala bwino.

“Mlimi akhonza kubwereza kupatsira mcherewu pakapita masiku 14 ndipo zimuchitira ubwino ndithu,” iye adatero.

Werengani pa tsamba 4 kuti mudziwe mmene mungawetere nkhumba.

Related Articles

Back to top button