Nkhani

Osataya za makolo

Listen to this article
  • Kulosera nyengo nkotheka

 

Pamene zikuoneka kuti ngozi zina zadzidzidzi zimene zakhala zikuchitika kaamba kolephera kulosera kubwera kwa ngozi zotere, boma lapempha Amalawi kuti alimbikire kugwiritsa ntchito njira za makolo polosera momwe mvula ingagwere. Pamene nkhani yolosera mvula ili mkamwamkamwa, boma lati lili pakalikiliki kuti madzi osefukira amene amasautsa m’madera ena chaka chino lisakhale vuto la mnanu.

Mumzinda wa Blantyre mudaoneka nkhokwe iyi
Mumzinda wa Blantyre mudaoneka nkhokwe iyi

Ambiri mwa anthu omwe amakhudzidwa ndi omwe amakhala m’mphepete mwa madzi makamaka m’maboma a kuchigwa cha Shire: Chikwawa ndi Nsanje. Chaka chatha kusefukira kwa madzi kudankitsa ndipo kudakhudza maboma 18 m’dziko muno, mpaka mtsogoleri wa dziko lino Peter Mutharika adati dziko lino ndi la ngozi, zimene zidachititsa kuti mabungwe ndi maiko athandizepo.

Malinga ndi mkulu wa nthambi yoona ngozi za dzidzidzi Bernard Sande, chomvetsa chisoni nchakuti ngozi zotere zikachitika boma limaononga ndalama za nkhaninkhani kusamala anthu okhudzidwawo ndi kubwezeretsa zinthu zoonongeka.

Chaka chino chokha

Koma bomalo lati sikuti likutaya njira za sayansi zolosera zanyengo.

Mlembi wa mkulu wa thambi yoona za ngozizi Bernard Sande adati ngozi zina monga kukokoloka ndi madzi osefukira zingapewedwe potsatira zizindikiro zachilengedwe. Iye adati kalekale makolo amalosera zobwera mtsogolo pogwiritsa zizindikiro zachilengedwe ndipo zimawayendera.

“Pali zizindikiro zina monga kalilidwe kambalame, mmene mitengo yayangira masamba ake, kaombedwe kamphepo ndi mmene kwatenthera kapena kwazizirira chaka chimenecho zomwe makolo amaloserera mmene mvula igwere,” adatero Sande.

Iye adatinso utawaleza ukaoneka kumwamba utazungulira mwezi kapena dzuwa zomwe ena amati nkhokwe, makolo amakhulupirira kuti chaka chimenecho kugwa mvula yambiri ndiye amakonzekera mokwanira.

“Lamulungu lapitali [pamwambo wokumbukira za ngozi zodza mwadzidzidzi] imodzi mwa nkhani zomwe zidakula ndi ya nkhokwe yomwe anthu ambiri omwe adalankhulapo adati ndi chizindikiro chakuti kubwera mvula yambiri,” adatero Sande.

Polankhula ndi Tamvani Lachitatu, T/A Maseya wa m’boma la Chikwawa adati nkhani yazizindikiro za kubwera kwa mvula yambiri ndi yoona ndipo zizindikirozi zimagwirabe ntchito mpaka pano.

Iye adati chaka chatha anthu ena kuchigwa cha Shire adadziwiratu kuti kubwera mvula yochuluka chifukwa kuoneka chigang’anthila (chinyama chooneka ngati ng’ona koma cha mlomo wautali).

Maseya adati chinyamachi chioneka ndi chizindikiro chakuti chaka chimenecho kugwa mvula yoopsa ndipo anthu amachitengera kwa amfumu omwe amadziwa kupha kwake.

“Zizindikiro zina ndi kutentha; kukatentha moonjeza timadziwa kuti kuvuta,” adatero Maseya.

Mfumuyo idavomereza kuti nkhokwe nayo ndi chizindikiro chakuti chaka chimenecho mvula igwa yamphamvu komanso zokolola zikhala zambiri.

 

Paramount Kyungu wa ku Karonga adati nthawi yodalira zizindikiro za makolo polosera kabweredwe ka mvula idapita ndipo masiku ano ndiwofunika kutsatira zomwe akatswiri a zanyengo anena.

Kyungu adati kalelo kudali anthu ake omwe amadalirika pankhani zoloserazo omwe           adamwalira kalekale choncho nkunamizana kunena kunena kuti anthu angadziwe zobwera pogwiritsa ntchito zizindikiro zachilengedwe.

Katswiri wa za sayansi ya za nyengo kusukulu yaukachenjede ya Chancellor College Cosmo Ngongondo adati zizindikiro monga nkhokwe zimachitika kaamba ka zochitika mlengalenga.

Iye adati sikuti zoterezi zikaoneka ndiye kuti ayembekezere mvula yambiri koma kuti mwamwayi zimangochitika kuti mvulayo yagwadi yambiri malingana ndi mmene mlengalenga mulili.

“Nkhokwe imaoneka kukakhala mitambo yomwe pa sayansi imatchedwa cirrus ndipo mitambo imeneyi siyibweretsa mvula koma chomwe chimachitika nchakuti mitamboyi imatsogozana ndi mtundu wa mphepo yomwe imabweretsa mvula.

“Pachifukwa ichi kumapezeka kuti mitambo ya Cirrus ija ikakhalako, mwayi wakuti mphepo yogwetsa mvula ikhalako umakula ndiye zikatero anthu amangoona ngati nkhokweyo ndiyo imabweretsa mvula yambiri,” adatero Ngongondo.

Iye adati nkhokwe imachitika pomwe kuwala kwa dzuwa kapena mwezi kwanjanja m’madzi ouma omwe amapezeka mmitambo ya cirrus ndipo kuwala konjanjako kumabalalika mmitundu yosiyanasiyana yomwe imakhala mmbalimmbali mwa dzuwa kapena mwezi.

Related Articles

Back to top button
Translate »