Chichewa

Osolola ndalama za Edzi mitima ili phaphapha!

 

Unduna wa zaumoyo wati zotsatira zakafukufuku wokhudza kusokonekera kwa ndalama zothandizira kulimbana ndi matenda a Edzi zatuluka, koma undunawu ukudikira ndemanga za nthambi yoona zakapewedwe ka matenda ya Centre for Disease Control (CDC) kuti unene tchutchutchu wake.

Mlembi wamkulu mu undunawu, Macphail Magwira, watsimikiza za nkhaniyi ndipo wati zotsatirazi azitulutsa mtsogolo muno n’kuwona kuti undunawu ungachitenji ndi anthu omwe akukhudzidwa ndi kusokonekera kwa ndalamazi.

“Zotsatira za kafukufuku zatulukadi koma zili m’manja mwa nthambi yoona zakapewedwe ka matenda osiyanasiyana kuti nawo aikepo ndemanga zawo. Zikachoka kumeneko, mpomwe tione kuti tingatani potengera zotsatira ndi ndemangazo,” adatero Magwira.

HIV

Iye adati pa anthu oganiziridwa onse, omwe adzapezeke olakwa adzaimitsidwa ntchito chifukwa chosokoneza ndalama za boma.

Kumapeto kwa chaka chatha, unduna wa zaumoyo udaimitsa ntchito anthu 63 zitadziwika kuti ndalama zina zomwe zimayenera kugwira ntchito yolimbana ndi matenda a Edzi zasokonekera ndipo undunawu umafuna nthawi ndi mpata wofufuzira.

“Tidaimitsa anthu ena omwe amaganiziridwa nawo. Ena mwa anthuwa amagwira kunthambi yowerengera ndalama za undunawu, makalaliki ndi ogwira ntchito m’maofesi ena kuti tifufufuze bwinobwino popanda zopinga,” adatero Magwira.

Anthuwa adapatsidwa mpaka pa 31 March chaka chino ngati tsiku lomwe angadzayambe ntchito koma mpaka pano anthuwa sadayambebe ntchito kudikira kuti zotsatira za kafukufukuyo zituluke.

Maunduna ndi nthambi zina za boma zakhala zikukhudzidwa ndi kusokonekera kwa ndalama za boma zomwe ena amangoti Kashigeti pofanizira ndi kubedwa kwa ndalama zankhaninkhani kulikulu la boma.

Kubedwa kwa ndalamazi ndi chimodzi mwa zifukwa zomwe zidapangitsa kuti maiko ndi mabungwe omwe amathandiza dziko la Malawi anyanyale ndi kuyimitsa thandizo lawo ponena kuti boma liyambe lakonza nyansi zonse kuphatikizapo kufufuza za ndalama zobedwazo. n

Related Articles

Back to top button