Chichewa

Pa Wenela pasintha zedi

Listen to this article

Tsikulo pa Wenela padali fumbi. Lazalo Watsika wabwera ndi moto ndithu.

“Abale inu, dzikotu ili limatembenuka zedi. Ndani ankadziwa kuti Lazalo n’kusankha anthu m’mipando yonona iyi? Ndani ankaganizako kuti tsiku lina iye ndi Male Chauvinist Pigs n’kukhala pachiongolero?” adafunsa Abiti Patuma.

“Ndipo sizinaoneke n’kale lonse kuti nduna zochuluka za mfumu zikhale zochuluka zimene zili ndi udindo umodzi basi. Apatu si zoti munthu yekha maudindo mbwee,” adayankhira Gervazzio.

Abale anzanga, pajatu pofuna kusangalatsa anthu susangalatsa onse.

“Koma apapa Lazalo ndiye walephera ndithu. Zoona mpaka kusankha anthu a mphasa imodzi kuti amuthandize kulongosola zinthu! Apapatu watidyetsa galu ndithu,” adatero mkulu adali ndi Abiti Patuma tsikulo.

“Pamenetu sindikumvetsa mpoti tsono kodi apa mumafuna kuti asankhe ndani? Ali dere n’kulinga utayenda naye. Tiyeni tidikire tione kuti zitha bwanji,” adatero Abiti Patuma.

Chiyembekezo cha anthu pa Wenela chidali chokwera ndithu.

“Tuvana wati? Apapa ena mukundinena kuti ndalakwitsa. Inde ndalakwa ndipo ndalakwa ndithu. Awa ndikuwapatsa ntchito ndipo akuyenera kuyendetsa bwino. Kupanda apo, pakutha kwa miyezi, ena awona chikwanje,” Lazalo adatero atafika malo aja timakonda pa Wenela.

Kunena zoona, Moya Pete ndimusowa. Komanso ndimusowa Atipatsa Likhweru, mnyamata wa miyambi.

“I am not my own mindful, if some of you have come straight from the land of darkness. Together we crumble and together we succeed,” adatero Chatsika.

“Komatu Vingerezi vanu muticheka navo. Tsono mukuti ife tizimvapo chiyani? Inuyo mukhala Martin Luther King Junior kapena Abraham Lincoln? Chonde tikhululukireni taweya,” adatero mkulu adali ndi Abiti Patuma.

Tsono pano pa Wenela zinthu zikusintha tsiku ndi tsiku, kuchita kusowa poyambira.

Adatulukira Saulo Walima atanyamula fayilo yake.

“Sindili pano kuchotsa munthu ntchito. Mudzichotsa nokha. Ena munandinyoza, munanditukwana. Lero ndikukupemphani, dzisanthuleni nokha ndipo mukapezeka kuti simukukwanira, chokani nokha basi,” adatero Saulo.

Ndidaona mayi wina amene amadziwa kulira kwambiri, Shad Black akuzyolika. Sindikudziwa kuti amakhumudwa ndi chiyani!

Nthawi imasintha. Pelete wafika. Batcha lalira.

Gwira bango, upita ndi madzi iwe!.

Related Articles

Back to top button