Chichewa

Pac ifuna mayankho pa za kukwera kwa mitengo

Listen to this article

 

Kukwera kwa zinthu m’dziko muno kwaika Amalawi pamoto wa mavuto zomwe zachititsa kuti bungwe la Public Affairs Committee (PAC) likonze msonkhano wopeza mayankho a mavutowa.

Mkulu wa bungweli Robert Phiri watsimikizira Tamvani za msonkhanowu koma wati tsiku ndi malo amsonkhanowu adziwitsidwa posakhalitsapa.

Kukweza kwa mitengo ya madzi ndi K45 pa K100 iliyonse, mitengo ya magetsi ndi K39 pa K100, shuga ndi K10 pa K100 iliyonse komanso zina zakudya ndi kukwera kwa chiongola dzanja choperekedwa munthu akakongola ndalama kubanki ndi zinthu zomwe zapangitsa kuti moyo ukhale wopweteka.

Msonkhano wa PAC mu 2012 kudali chitetezo chokhwima zedi
Msonkhano wa PAC mu 2012 kudali chitetezo chokhwima zedi

Izi ndi zomwe si zidakhazike chete bungwe la PAC pamene akonza nkhumano kusaka mayankho.

“Bungwe la PAC likudziwa nyengo zowawitsa zomwe Amalawi akudutsamo. Chomwe tikufuna nchakuti Amalawi tikhale pamodzi kuti tipeze mayankho pa mavutowa,” adatero Phiri.

Titamufunsa ngati msonkhanowo ungabale zipatso, Phiri adati iwo akukhulupirira kuti ukhala ndi chophula kusiyana nkuti aliyense azizilankhula payekha.

“Padakalipano tikulumikizana ndi mabungwe komanso mbali zina momwe tingakonzere msonkhanowu komanso momwe tingapezere mayankho ku mavuto amene tikukumana nawowa,” adatero Phiri.

Iye adaonjeza kuti: “Zomwe mabungwe ndi anthu onse adzagwirizane ndi zomwe zidzachitidwe chifukwa ife kwathu ndi kupereka mwayi kuti anthu akambirane ndi kupeza mayankho.”

Bungweli lidachititsanso msonkhano wotere mu March 2012 pamene kudali chitetezo chokhwima pamene ena amati msonkhanowo udali ndi cholinga chofuna kuthana ndi boma.

Msonkhanowu womwe mbali ya boma sidafikeko, udachitikira ku Limbe Cathedral mumzinda wa Blantyre.

Koma Phiri wati msonkhano ukudzawu umemeza mbali zonse kuphatikizapo a boma chifukwa bungwe lawo limapereka kumva kwa boma lililonse lomwe likulamula.

Koma mkulu wa bungwe loona ufulu wa ogula la Consumer Association of Malawi (Cama) John Kapito wati boma lakhumudwitsa Amalawi chifukwa cholephera kukonza zinthu.

“Panopa zinthu zaipa ndipo zasokonekera, makuponi kulibe, chiongola dzanja chakwera ku mabanki zomwe zichititse kuti katundu akwere zomwe zizunze Amalawi. Zomwenso boma likuchita sizikuoneka ndipo tilibenso chiyembekezo ngati zinthu zibwerere mchimake,” adatero Kapito.

Iye adati Amalawi akuyenera kumadya mosinira komanso amange malamba chifukwa komwe tikupitaku zinthu zinyanya kuwawa.

Koma mtsogoleri wa dziko lino Peter Mutharika Lachinayi adati mavuto amene dziko lino likukumana nawo sadayambe aonekapo ndipo adati ndi bwino Amalawi akhale pamodzi kuti apeze mayankho. n

Related Articles

Back to top button
Translate »