Nkhani

‘Palibe angamange mvula, siyani kuzunza anthu’

Listen to this article

Masiku apitawa anthu 7 adawagwira ku Chiradzulu ndipo adawazunza powaganizira kuti akumanga mvula. Adawakolezera moto masanasana kuti aothe ndipo akuti anthuwo atangonena kuti mvula ibwera, adawasiya ndipo mvula ikulikitika mpaka lero. Kodi munthu angathe kumanga mvula? Nanga amamangira chiyani? BOBBY KABANGO akufunsa mneneri wa zanyengo Elina Kululanga kuti afotokoze zomwe zimachitika kuti mvula igwe kapena isagwe madera ena motere:

RAINING
RAINING

Pali zikhulupiriro zoti mvula ikamavuta, monga yavutira chaka chino maka madera a chigawo chakummwera, ndiye kuti ena akuimanga dala. Inu monga a zanyengo mukuti bwanji?

Ayi, ndipo sizingatheke munthu kumanga kapena kugwetsa mvula.

Nanga mvula ikuvuta chonchi bwanji?

Iyi tsopano ndi nkhani ya kusintha kwa nyengo. Mpweya woipa womwe tikulandira ndiwo ukuchititsa kuti mvula ikhale yovuta chonchi. Nkhani iyi ndi ya dziko lonse komanso maiko ena akukumananso ndi vutoli, si kuno ku Malawi kokha, ayi.

Kodi zatani kuti chaka chino tikumane ndi mavutowa?

Nkhani ndi kusintha kwa nyengo. Kuti mumvetse chomwe chikumachitika ndi ichi: mitambo ikumakungana bwinobwino kusonyeza kuti mvula ibwera. Mphepo yoipa ikangowomba, basi mvula singabwerenso ngakhale mitambo itachuluka maka.

Kodi kale lonse mphepo imeneyi idali kuti?

Mumvetsetu, ndati kusintha kwa nyengo, kalelo chilengedwe chidali chonse, koma pano chilengedwe chasokonekera.

Ndiye mukukana kuti wina sakumanga?

Osatheka, ndipo padziko lapansi palibe ngakhale sing’anga kapena mfiti yodziwa motani amene angamange mvula.

Anthu amene adawagwira ku Chiradzulu adauza gulu kuti mvula igwa mawa lake ndipo zidatheka, ndiye mwati awawa mvula sadaimange?

Inuyo mumamvera za nyengo? Chifukwa sabata yatha takhala tikulengeza kuti sabata ino yonse mvula igwa kwambiri kuchigawo cha kummwera, ndiye mukudabwanso pamene mwaona mvula ikubwera?

Bwanji mvula ikumabwera mudzi umodzi wina osabwera poti ndi pafupi?

Izi ndiye zomwe zikutsimikiza kuti nyengodi yasintha, apopo ndiye kuti pakukutanthauzirani kuti mphepo yoipayo idakhudza mbali ina kwina ayi.

Inuyotu mwakhalapo kumudzi, monga kalelo simumakhulupirira kuti anthu amamanga mvula?

Ndinkakhulupirira, koma nditabwera kunthambi ya zanyengo ndi kuona momwe zimakhalira kuti mvula igwe, ndidadziwa kuti ndinkadzinamiza.

Ndiye kuti inuyo azanyengo mumamanga mvula, eti?

Ayinso, ifeyo timangoona momwe mphepo ikuyendera ndipo kuti kuyenda kwake kukutanthauza chiyani. Tikaona ndi pamene timalengeza momwe mvula ibwerere komanso momwe kutenthere ndi kuzizira komwe.

Mutani kuti anthuwa akhulupirire kuti munthu sangamange mvula?

Azimvera wailesi momwe zanyengo zikuyendera komanso azitifunsa. Tikhalanso ndi nthawi yowaphunzitsa anthu za nyengo mwezi umenewu.

Ngati wina akuti amatha kumanga mvula, mumutani?

Ndatitu palibe amene angathe, koma ngati ena akutero ndiye abwere kuno adzatitsimikizire.

Nanga mphenzi yokha ndiye munthu angapange?

Ayinso, izo ndi bodza. Palibe angapange mphenzi ndipo sadzapezekapo. Zonse ndi zokhudza chilengedwe.

Related Articles

Back to top button
Translate »