Nkhani

Panazale samakololapo!

Flames yalepherana mphamvu ndi Swaziland 2-2 kusonyeza kuti m’gulu L la mpikisano wolimbirana chiko cha Africa Cup of Nations (Afcon) Malawi ili panambala 3 ndi pointi imodzi m’masewero awiri itagonja pakhomo ndi Zimbabwe m’masewero oyamba mu June.

Kochi Ernest Mtawali akukhulupirira kuti Flames ichitabe bwino mu Afcon pamene yatsala ndi masewero anayi.

Kudabwitsa kwake n’koti iye akugwiritsa ntchito osewera amene ndi apanazale. Kodi a kochi, panazale amakololapo?

Osewera mukugwiritsa ntchitowa sangatibweretsere zotsatira lero ndi lero. Ngakhale dziko la Malawi ndi la njala ndi kupambana, bwana Mtawali mungotilimbitsa mtima ponena kuti mumpikisanowu tituluka.

Mukadafuna zokolola bwezi mutatenga achina Esau Kanyenda kuti akathandize ntchito anawa kutsogoloko. Pamene Micium Mhone adavulala, ife timayembekeza kuti Robert Ng’ambi alowetsedwa.

Naye Gerald Phiri Jnr adaonetsa kuti akutopa chigawo chachiwiri chija zomwe zimafunika kuti Frank Banda agwire ntchito. Koma mudakhulupirira ana aja ndiye mukuganiza kuti tidakakololapo?

Tikakhala ife aganyu ndiye sitidamvere nawo mpirawo. Pajatu m’zipatala mulibe mankhwala ndiye Flames yanuyo ikatikweza BP tipita kuti?

Kumbukirani malangizo a achipatala poonera Flames: Chonde onetsetsani kuti BP yanu mwayezetsa bwinobwino popewa kutifera. Gulani kabotolo ka Panado popewa mutu waching’alang’ala. Gulani thanzi ORS popewa m’mimba mwa mpezepeze ndi mothulula. Ngati mukuonera usiku, onetsetsani kuti mwagula mankhwala ogonetsa.

Amayi pempheranitu ndalama ya ndiwo kwa amuna anu. Mwana asayandikire bambo ake gemu ikatha. Musayandikane ndi madzi otentha. Musayandikire zinthu zosweka. Musakhale pafupi ndi mbaulae.

Related Articles

Back to top button