Chichewa

Pewani chipalamba posamala mitengo

Listen to this article

 

 

Kampani yogula fodya ya Limbe Leaf Tobacco Company yati makolo azitsogolera ana pantchito yobzala mitengo kuti m’dziko muno musadzakhale chipalamba chomwe chingabweretse mavuto adzaoneni.

Mkulu wa bungweli Rodney Haggar adanena izi Loweruka pomwe kampaniyi inkapereka mbande za mitengo pasukulu ya pulayimale ya Mwakhundi kwa T/A Khongoni m’boma la Lilongwe.

Haggar adati kutsogoza achinyamata pantchito zobwezeretsa chilengedwe kungathandize kuti achinyamata azikula ndi mtima wozindikira kufunika kosamala chilengedwe kuti mtsogolo muno mavuto a kusintha kwa nyengo adzachepe.

Iye adati vuto lalikulu ndi loti anthu ambiri amakanika kusamala mitengo yobzalabzala uku ali yakaliyakali kudula mitengo yachilengedwe, zomwe zimachititsa kuti mabweredwe a mvula asinthe komanso kunjaku kuzitentha mopitirira muyeso.

Achinyamata azikula ndi mtima wosamala chilengedwe
Achinyamata azikula ndi mtima wosamala chilengedwe

“Mitengo mwalandirayi muisamale kuti ikule komanso musalekere pomwepa, ayi. Pezani mitengo yambiri ndipo paliponse pomwe palibe mitengo mubzalepo mitengo. Tayesetsaninso kutsogolera achinyamata pantchito yobzala mitengo kuti akamakula azikhala ndi malingaliro obwezeretsa chilengedwe,” adatero Haggar.

Mkuluyu adati mitengo ndi yofunika pantchito zosiyanasiyana makamaka nkhani zaulimi ndipo kulekerera pantchito yobzala mitengo n’kuweta chipalamba chomwe zotsatira zake zingadzaike Malawi pamoto.

Mkulu wa bungwe la mgwirizano wa mabungwe a zaulimi Tamani Nkhono-Mvula adagwirizana ndi maganizo olimbikitsa achinyamata kukula ndi mtima wosamala chilengedwe.

“Nkhani yaikulu apa ndi kumanga maziko oti mtsogolo muno zinthu zisadzavute. Chilichonse panopa pankhani ya ulimi chikudalira mitengo. Kuti mvula igwe molongosoka ndi mitengo; nthaka ndi iyi mukuyiona nokha ikungokokolokayi chifukwa chosowa chitetezo; kutentha ndiye n’kosayamba,” adatero Nkhono-Mvula.

Dzinja lililonse kumakhala nthawi yobzala mitengo koma mvula ikatha mitengo yambiri imafota n’kuuma chifukwa chosowa chisamaliro.

Mitengo ina imapsa ndi moto wolusa womwe anthu ena amayatsa mosasamala chifukwa chosazindikira kufunika kosamala mitengo ndipo izi zimatchititsa kuti chaka ndi chaka mitengo izibzalidwa malo amodzimodzi.n

Related Articles

Back to top button