Chichewa

Pezani umuna wa ng’ombe

Listen to this article

 

Nthawi yokhala ndi ng’ombe za makolo yapita. Ndi K1 500 yokha, alimi akhoza kupeza umuna wa ng’ombe za makono.

Zonse zikutheka kusukulu ya zaulimi ya Mikolongwe komwe kukupezeka mbewu za ng’ombe zamkaka za Friesian Holstein. Ndiye palinso mtundu wa nyama ya ng’ombe zamkaka za Brahman zomwe ndi za mtundu wa nyama ndi mtundu wa Jersey zomwenso ndi za nyama komanso mkaka zimatulutsa wambiri. Malinga ndi yemwe amayang’anira nthambi yosunga umuna wa ng’ombe kusukuluyo, Innocent Mboma, njira yogula umuna ndi yachidule, yosamala komanso yotchipa ndipo alimi akuyenera kutsatira njirayi ngati akufuna mitundu ina ya ng’ombe.

 

James Molende kukolola umuna kwa ng’ombe ya mtundu wa Friesian
James Molende kukolola umuna kwa ng’ombe ya mtundu wa Friesian

Madera ambiri kuti ugule ng’ombe ya mphongo, mtengo wotsikitsitsa ndi K150 000 ng’ombe imodzi mtengo woti mlimi sangakwanitse.

“Nchifukwa chake tikugulitsa umuna kuti alimi asavutike. Umuna wa K1 500 wokha angathe kukakweretsa ng’ombe imodzi ndipo ndi kamodzi kokha ng’ombe yatenga bele,” adatero a Mboma. Iwo adati umunawu ungakweretsedwe kwa ng’ombe ya mtundu ulionse ndipo mwana amene akabadweyo akakhala wa mtundu wa umuna omwe adagula.

“Kaya ng’ombe yake ndi ya mtundu wanji, umuna umenewu ukagwirabe ntchito. Ndipo mwana wobadwayo adzatenga bambo ake.”

Iye adati umuna umatengedwa Lolemba ndi Lachinayi sabata iliyonse ndipo alimi angathe kupita kusukuluyo tsiku lililonse ndipo umunawo akaupeza.

“Pobwera akuyenera kutenga potengera monga fulasiki kuti umunawo usafe. Komanso si kuti alimiwa timangowagulitsa, timawaphunzitsa momwe angasungire komanso momwe angakweretsere ng’ombe yawo,” adatero a Mboma.

Iwo adati patsiku amakolola umuna wochuluka ndi mamililita 10 kwa ng’ombe imodzi ndipo akaugawa angathe kukweretsa ng’ombe zazikazi pafupifupi 100.

Ntchitoyo akuti adayiyamba zaka ziwiri zapitazo koma alimi ena adali asadadziwe kuti angathe kugula umunawu kuchokera ku sukuluyi

Related Articles

Back to top button