Chichewa

Phindu kawawa ndi ulimi wa tsabola

Listen to this article

 

Akulipirira ana awiri ku sekondale; wagula mbuzi 19 ndi nkhuku 30. Njinga, ziwiya za pakhomo komanso banja lake silikugona ndi njala. Nkhani ya Jimmy Maliwu, mlimi wa tsabola ku Mulanje ndi chitsanzo kuti ulimi wa tsabolawu ndi kawawa. BOBBY KABANGO akucheza ndi mlimiyu:

Maliwu: Ndidagulitsa mosavuta

Wawa achikumbe…

Wawa, imani komweko musafike pafupi, kuno ndi kwa alimi okhaokha.

Kuli chiyani mukuchita kukanizira?

Tikusankha tsabola ndiye mphepo yake inuyo simungayandikire, mukuona aliyense akungoyetsemula.

Ndiye tidziwanetu…

Ndine mlimi wa tsabola, dzina ndine Jimmy Maliwu wa m’mudzi mwa Sazola kwa Senior Chief Mabuka m’boma la Mulanje.

Mudayamba liti ulimiwu?

Mu 1999 ndi pamene ndidayamba kulima tsabola.

Chidachitika nchiyani kuti muyambe ulimiwu?

Pa nthawiyo n’kuti ndikulima chimanga komanso mbewu zina. Ndiye ndinkafuna ndichite ulimi wina womwe ndizipezerapo ndalama. Apa ndi pamene ndidasankha tsabola.

Chifukwa chiyani mudasankha ulimi wa tsabola?

Ndinkafuna ulimi wa fodya, koma kuno sachita bwino. Ulimi wa tsabola ndi omwe ndidaona kuti akuphamo ndalama.

Mudayamba bwanji?

Ndidalima mizere yochepa, ndimafuna kuti ndione ngati ndingathe komanso ngati msika wake uchite bwino. Zidayenda koma osati kwambiri, ndidaikamo chidwi.

Chidayenda nchiyani?

Kumunda zidatheka komanso pamsika ndidagulitsa mosavutika ngakhale mtengo wake udali wolira.

Mtengo udali bwanji?

Ndidagulitsa K39 pa kilogalamu pamene alimi ena amagulitsa K50.

Kuchoka 1999 kufika lero, ulimiwu ukuyenda bwanji?

Mitengo ndiyo yakhala yovuta koma kumunda ndiye zonse zili bwino. Ndidaonjezera munda ndipo pano ndikulima wokula ndi mamita 35 mulitali ndi 17 m’lifupi.

Munda umenewu mukukolola wochuluka bwanji?

Ndikumapeza tsabola makilogalamu 150 ngati mvula yagwa bwino komanso ngati matenda sadafike.

Chaka chatha zidayenda bwanji? Nanga pamsika padali bwanji?

Chaka chatha ndidakumana ndi vuto la matenda ndiye ulimi udavuta moti ndidapeza makilogalamu 45 okha chifukwa alangizi adafika mochedwa. Pamsika ndiye zidali bwino chifukwa amagula K2 500 pa kilogalamu.

Ndi matenda ati amene adavuta?

Tsabola amapanga zilonda komanso mitengo imauma. Zikatere zimakhala zovuta kuti abereke bwino. Panopa matendawa tawakonzekera chifukwa tidali ndi maphunziro a momwe tingathanirane ndi matendawa. Koma vuto lomwe lidalipo kuti tikumane ndi matendawo nchifukwa cha manyowa amene tidagwiritsira ntchito.

Tsabola wakupindulirani bwanji?

Muli ndalama, chaka chatha ndidapeza K112 500 kuchokera m’makilogalamu 45 amene ndidakolola. Ndagula mbuzi 19 komanso nkhuku 30. Ndili ndi ana atatu, mmodzi ali Fomu 2 wina 4 ndi wina ali ku pulaimale. Onsewa ndalama zake zikuchokera mu tsabola. Sindinagonepo ndi njala chifukwa ulimiwu umandisuntha.

Tifotokozereni za kumunda, kuli bwanji pano?

Panopa tikuwokera pamene mitengo ya chaka chatha tikuthyolera kuti ipange nthambi.

Mukulima tsabola wanji?

Chiyambireni ndimalima tsabola wa kapiripiri ndipo ndimagulitsa kukampani ya Zikometso m’boma lomwe lino. n

Related Articles

Back to top button
Translate »