Sunday, May 29, 2022
  • About Us
  • ImagiNATION
  • Adverts
  • Rate Card
  • Contact Us
The Nation Online
Advertisement
  • Home
  • News
  • Politics
  • Business
  • Entertainment
  • Life & Style
    • Every Woman
      • Soul
      • Family
    • Religion
    • Feature
  • Society
  • Columns
  • Sports
  • Chichewa
  • Enation
No Result
View All Result
  • Home
  • News
  • Politics
  • Business
  • Entertainment
  • Life & Style
    • Every Woman
      • Soul
      • Family
    • Religion
    • Feature
  • Society
  • Columns
  • Sports
  • Chichewa
  • Enation
No Result
View All Result
No Result
View All Result
Home Chichewa

Phindu la kusankhiratu fodya pothyola

by Nation Online
13/03/2021
in Chichewa
3 min read
0
Share on FacebookShare on TwitterShare on WhatsAppShare on LinkedinLinkedinShare via Email

Mlimi akasankhiratu fodya wake  pamene akuthyola, kusoka  ndi kuumitsa, amapeza phindu lochuluka kusiyana ndi kumangomusakaniza ndi kudzasankha atamuumitsa kale.

Alangizi akuti izi zili chomwecho chifukwa zimathandiza kuti mlimi aike fodya wofanana  m’belo limodzi ndipo sasemphanitsa.

Zotsatira zake, mlangizi wa mbewuyi ku bungwe la Agriculture Ressearch and Extension Trust (Aret) Maurice Mantchombe adati mlimi amagulitsa pa mtengo woyenera komanso amapulumutsa ndalama zimene amayenera kuononga akamubweza kuti akayambirenso kusankha.

“Kusankhiratu kumathandiza kuti  fodya akhale wofanana  mtundu, kutalika ngakhale  michere yake chifukwa sasakanikirana.

Kusankhiratu fodya pothyola ndi kopindulitsa

“Zotsatira zake, amakhala pamlingo umene ogula amafuna choncho mlimi amapeza phindu lochuluka,” iye adatero.

Mantchombe adaonjeza kuti fodya wotereyu savuta kuumitsa chifukwa cha kufananaku.

Iye adati chifukwa choti amamupatula, chisamaliro chimakhala chabwino choncho sapezeka ndi zinyalala.

Mlangiziyu adati mlimi  amadzichepetsera ntchito ndi nthawi chifukwa akauma, savutika ndi kusankha.

Iye  adati njirayi imathandizira kuti fodya wapansi yemwe amakhala ndi dothi, asaipitse wapakati kapena wapamwamba.

“Ogula amadziwa kuti fodya wapansi amakhala wa matope choncho akakhala m’belo lake, mlimi amagulitsa molingana ndi mtengo wa fodya wa geledi imeneyo pa msika.

“Mlimi akasoka kapena kuumitsa pamodzi  fodya wotereyo ndi wabwino, yense amaipa ngakhale atamusankha choncho  amamugulitsa pa mtengo wotsika ngati omwe akadagulitsira wa pansi,” adafotokoza motero.

Mlimi wina wa  fodya wa m’boma la Kasungu David Nekhantani adati kusankhiratu fodya pomwe akuthyola kumamuthandiza kugulitsa mwachangu komanso pa mtengo wabwino.

Iye adati mitengo ya fodya kumsika imasinthasintha makamaka nyengo yogulira ikamapita kumapeto choncho amamaliza mwachangu chifukwa sataya nthawi ndi kumasankha atauma kale.

“Kusankha fodya woti wauma kale ndi ntchito yofuna nthawi yaitali chifukwa kumalira kuti ugwire tsamba lililonse. Izi zimapangitsa kuti mlimi amalize mochedwa  mapeto ake, amakapeza misika itapenga,” iye adatero.

Lackson Chikwapulo yemwe amachitanso ulimi wa mbewuyi m’boma la Chirazulu adati kupatula kupindula adazindikira kuti njirayi ndi yophweka kusiyana ndi kusankha atauma kale.

Iye adati amangoonetsetsa kuti pa tsiku azithyola masamba awiri oyang’anizana pa mtengo uliwonse wa m’mundamo.

Akachoka apa, mlimiyu adati amamusoka, kumuyanika, kumusunga, kumumanga ndindi ndi kumudindira pamodzi.

“Timachita izi pa masamba awiri alionse a fodya omwe takhala tikuthyola m’mundamo osawasakaniza,” iye adatero.

Mantchombe adakumbutsa alimi kuti akuyenera kusamala ndi zinthu monga ulusi wa masaka, mapepala  ndi nthenga za nkhuku pamene akuthyola ndi kuumitsa chifukwa zimamata ku fodya.

Popewa izi, iye adati mlimi asanyamulire fodya wake m’thumba la saka kapena pepala pamene akuchoka naye kumunda.

Mlangiziyu adati zoterezi zimavuta kuziona ngakhale mlimi asankhe choncho zimakaonekera kumsika.

“Fodya akakhala wamuwisi, amakhala ndi mafuta omwe amachititsa zinthu monga ulusi wa matumba, mapepala ndi nthenga za nkhuku, zizimatirira mosavuta,” iye adatero.

Chifukwa cha ichi, iye adati ndi bwino kuti alimi azigwiritsa ntchito zinthu monga madengu, ngolo ndi zina zomwe sizingamatirire ku fodya.

Kuonjezera apa, mlangiziyu  adati mlimi akuyenera kutetezera m’chigafa momwe akuyanika fodya wake ku zinthu monga nthenga za nkhuku pamene akuyanika fodya.

Previous Post

Sports Council summons FAM

Next Post

Katemera wa covid ayamba

Related Posts

Nkhani

Woimba abedwa mumzinda wa mzuzu

May 28, 2022
Nyumba ndi katundu zambiri zidawonongeka ndi Anna komanso Gombe
Nkhani

K34.8 biliyoni ya ngozi zadzidzidzi

May 28, 2022
Nkhani

Agwidwa ndi yunifomu za polisi

May 22, 2022
Next Post
President Lazarus Chakwera took his jab publicly to demystify Covid-19 vaccines

Katemera wa covid ayamba

Opinions and Columns

Off the Shelf

Poor timing of Aggreko decommissioning now hurting

May 28, 2022
My Diary

Corruption as an elephant

May 28, 2022
Business Unpacked

Tame egos, take risks to grow economy

May 26, 2022
People’s Tribunal

What was that press briefing all about?

May 22, 2022

Trending Stories

  • People travel on the first part of the East Bank road from Thabwa

    K14bn road fund down the drain

    0 shares
    Share 0 Tweet 0
  • ACB sleeps on Bingu’s wealth investigation

    0 shares
    Share 0 Tweet 0
  • Acb explains Sattar miss

    0 shares
    Share 0 Tweet 0
  • RBM justifies devaluation stance

    0 shares
    Share 0 Tweet 0
  • Bullets , Silver Strikers renew rivarly

    0 shares
    Share 0 Tweet 0

Malawi-Music.com Top10

  • Values
  • Our Philosophy
  • Editorial policy
  • Advertising Policy
  • Code of Conduct
  • Plagiarism disclaimer
  • Disclaimer
  • Privacy Policy
  • Terms of use

© 2022 Nation Publications Limited. All Rights Reserved.

No Result
View All Result
  • Home
  • News
  • Politics
  • Business
  • Entertainment
  • Life & Style
    • Every Woman
      • Soul
      • Family
    • Religion
    • Feature
  • Society
  • Columns
  • Sports
  • Chichewa
  • Enation

© 2020 Nation Publications Limited. All Rights Reserved.

This website uses cookies. By continuing to use this website you are giving consent to cookies being used. Visit our Privacy and Cookie Policy.