Nkhani

Phoya amyula maliro aweni, apepesa Achewa

Listen to this article

Mkonze mkonze adamyula maliro aweni. Izi mzomwe phungu wa nyumba ya malamulo Henry Phoya anachita msabatayi.

 

Imvani izi: mkulu wa bungwe la Achewa la Chewa Foundation Heritage (Chefo), Dr Justin Malewezi wati ndiokhutira ndi kupepesa kwa nduna ya zamalo yemwenso ndi phungu wa chigawo cha kum’mawa kwa boma la Blantyre, Henry Phoya.

Phoya adatsutsula Achewa pachilonda pomwe amalandiridwa kuchipani cha People’s Party pa 28 pomwe adati sadalandiridwe kuchipani cha MCP pomuuza kuti akuyenera amete.

Iye adati atafika kuchipani cha MCP adauzidwa kuti ngati akufuna akhale ndi malo m’chipanicho akuyenera avinidwe gule wamkulu.

Mawuwa adayabwa mafumu a mtunduwo omwe akuti amatchaira lamya akuluakulu abungwe la Chefo kuti atsate nkhaniyo.

Lolemba pa 30 Epulo, bungweli lidapempha Phoya kuti apepese Achewa chifukwa chipani cha MCP sichiimira Achewa ndipo siiwo adachiyambitsa.

Malewezi adati ndikulakwa kuphatikiza nkhani za ndale ndi mtundu kotero ngati Phoya sangapepese ndiye kuti nkhaniyo aitengera pena.

Lachiwiri pa 1 Meyi Phoya adapepesa kwa Achewa ndipo adati ngati akupemphedwa kuti mawuwo adalakwira chikhalidwe ndiye sangakane kupepesa.

Phoya adati ngati omwe akumupempha kuti apepese akulankhulira nkhani za ndale ndiye kuti akulakwitsa chifukwa iye sadanene kuti iye ali ndi umboni pazomwe adalankhulazo.

“Anthu akuyenera kumvetsa, ine ndidanena kuti alipo omwe adandiuza zimenezo osati kuti ine ndidali nazo umboni.

“Mumadziwa moyo wanga ndipo ndilinso ndi abale anga omwe ndi Achewa,” adatero Phoya.

Related Articles

Back to top button
Translate »