Chichewa

Phwitiko: Kutambasula za maphunziro

Listen to this article

Unduna wa zamaphunziro udalonjeza zotukula maphunziro m’dziko muno. Poyesetsa kukwaniritsa izi, undunawu uli ndi mapologalamu osiyanasiyana. M’miyezi yapitayi undunawu udakonza zokweza fizi kuti uzitolera ndalama zokwanira zotukulira maphunziro. STEVEN PEMBAMOYO adacheza ndi mneneri wa undunawu Rebecca Phwitiko:

Phwitiko: Ndimalumikiza  unduna ndi atolankhani
Phwitiko: Ndimalumikiza
unduna ndi atolankhani

Tafotokoza mbiri yako.

Ndine Rebecca Phwitiko, ndidabadwira ndi kukulira mumzinda wa Blantyre koma ndimachokera m’mudzi mwa Danda, T/A Kalumbu m’boma la Lilongwe.

Nanga mbiri ya maphunziro ako ndiyotani?

Ndidaphunzira kusekondale ya Our Lady of Wisdom ku Blantyre m’zaka za 1999 mpaka 2002 kenako n’kukapanga maphunziro a ukachenjede ku Chancellor College. Panopa ndikuonjezera maphunzirowa kuti ndikhale ndi Masters Degree.

Udindo wako weniweni ku Unduna wa zamaphunziro ndi wotani?

Kwenikweni ntchito yanga ndi yokhudzana ndi zofalitsa nkhani za undunawu. Ntchito yokonza zokhudza uthenga wopita kwa anthu, kulumikiza unduna ndi nyumba zofalitsa ndi kusindikiza nkhani, kukonza zochitika za unduna ndi kusanthula zomwe olemba ndi kufalitsa nkhani alemba ndi kulandira madandaulo ochokera kunthambi zosiyanasiyana ndi zina mwa ntchito zanga.

Usadalandire udindo umenewu unkagwira ntchito yanji?

Ndinkagwira ntchito kuwayilesi ya boma ya Malawi Broadcasting Corporation (MBC) ngati mkonzi wa mapologalamu, muulutsi ndi mtolankhani.

Umagwiritsa bwanji ntchito nthawi yako yapadera?

Ndikakhala ndi mpata ndimakonda kuwerenga mabuku okamba za Africa. Ndimakondanso kumvera nyimbo ndi kuyenda kuona malo osiyanasiyana.

Unduna wa zamaphunziro umanena kuti cholinga chake choyamba nkutukula maphunziro. Kodi mukuchitaponji pofuna kukwaniritsa zimenezi?

Choyamba unduna wa zamaphunziro uli ndi udindo waukulu kuphunzitsa mtundu wa Amalawi. Udindo umenewu timagwirira ophunzira, aphunzitsi, makolo ndi ofalitsa komanso kusindikiza nkhani. Pofuna kukwaniritsa izi, tili ndi mapologalamu ambiri koma kuti onsewa atheke, mpofunika mgwirizano waukulu pakati pa ife ndi magulu onse omwe ndatchulawa ndipo mzati wake nkulumikizana pafupipafupi komanso moyenerera.

Koma ukuona kuti mukhoza kukwaniritsa masomphenya amenewa?

Unduna wathu sungapume pokhapokha masomphenyawa atakwanitsidwa chifukwa mtundu wosaphunzira sungatukule dziko. Nthambi zonse za chitukuko monga ulimi, zaumoyo, zachuma, mabizinesi ndi zina zonse zimayenda chifukwa cha maphunziro apamwamba. n

Related Articles

Back to top button