Chichewa

Phyzix wadza ndi Captain Long John

 

Patapita zaka zingapo akutchuka ndi nyimbo zomwe zidavuta monga Cholapitsa, Gamba, Chilombo, Abwana, Memba, Town Monger, Man phyzo, Handsome, The Leasder ndi Gamba wa Suit, Noel Chikoleka, yemwe amadziwika kuti Phyzix pankhani zoimba, wadzanso ndi chimbale china  chotchedwa Captain Long John. Monga mwachizolowezi nyimbo za mkuluyu zimakhala ndi chikoka. STEVEN PEMBAMOYO adacheza naye zokhudza chimbale chatsopanochi motere:

Ndikumbutsane dzina lija…

Phyzix: Muyembekezere chimbale  cha nyimbo zothyakuka
Phyzix: Muyembekezere chimbale
cha nyimbo zothyakuka

Dzina langa ndi Noel Limbani Jack Chikoleka, ndimachokera m’mudzi mwa Mwamadi, T/A Kambwiri m’boma la Salima. Dzina lodyera ndine Phyzix.

Ulipa uli ndi zimbale zingati za nyimbo?

Chiyambireni kuimba ine ndatulutsapo zimbale 5 koma zitatuzo ndimangotulutsira pamakina a internet ofuna amagulira pamenepo nyimbo zanga. Chimbale chomwe ndidatulutsa n’kumwaza pamsika chidali chomwe ndidatulutsa m’chaka cha 2005 chomwe chidali ndi nyimbo ya Cholapitsa. Nthawi imeneyo ndili ku Mzuzu University.

Pano ukumveka kuti ukutulutsa chimbale china, chimenechi ndi chimbale chanji?

Chimenechi ndi chimbale chomwe ndikuchitcha Captain Long John ndipo chili ndi nyimbo 10. Nyimbo 6 zatuluka kale ndipo zina zotsalazo zituluka nthawi ina iliyonse kuti anthu asangalale ndi nyimbo zina zophikidwa bwino.

Chimbale chimenechi chituluka motani?

Chimbale chimenechi chituluka mwaluso lapadera. Poyamba, nyimbo zonse zizituluka ngati ma singles (imodziimodzi) ndipo zonse zikhala ndi wowonerera zomwe. zonse zikadzatha ndidzakhazikitsa chimbale kuti anthu azidzatha kukhala nacho ndi kumvera kuyambira nyimbo yoyamba mpaka yomaliza chifukwa ndikudziwa kuti akangomva imodzi pawayilesi kapena kuona pakanema azikhala ndi njala yaikulu yoti amvereso inzake pokhapokha chimbale chonse chidzathe mpomwe anthu adzakhale ndi mwayi wotere.

Uthenga munyimbo za m’chimbalechi ndi wotani?

Muli uthenga osiyanasiyana, monga munyimbo ya Ndekha muli uthenga wa chisangalalo cha ukwati. Ndidaipeka makamaka polemekeza ukwati wanga koma ndidaimba moti anthu enaso akhoza kuigwiritsa ntchito polemekeza ukwati wawo. Mfana Wolusa ndi munthu wachangu patauni osafuna kulekerera kanthu ndipo ndi nyimbo yokoma kwambiri. Baby OldSkool ndi nyimbo yomwe imakamba za mkazi wotsogola, odziwa zambiri zakale ndi zatsopano. Mkaziyu ali ndi chikoka koma amachititsa mantha kumufikira ndiye mkatimo ine ndikuyesa kumufikira. One Meets Two imatanthauza kukumana kwa ine ndi akadaulo anzanga Marcus ndi GD, omwe akhala akundithandiza munyimbo zambiri ndipo ndikupitirira kwa nyimbo ya Lone Ranger. Kwa omwe amatsatira Lone Ranger akhoza kukhala ndi chithunzithunzi cha nyimbo yatsopanoyi. Nyimbo zinazo sizidatuluke koma nazoso zili ndi uthenga wapamwamba kwambiri moti anthu adzazikonda zikatuluka.

Tangotiuza momwe udabwerera muzoimbazi?

Nthawi yomwe ine ndimayamba kuimba, oimba chamba cha Rap tidalipo ochepa kwambiri ndipo nyimbo ikatuluka imakhala nthawi yaitali isadalowe pansi. Pang’onopang’ono ena adayamba kubweramo koma panthawiyo kudali kovuta kupeza mwayi wa makina a internet zomwe zinkatipangitsa enafe kuti tizisowa njira zopititsira patsogolo luso lanthu.

Panotu kuli makina a internet mbweee, ukupindulapo motani?

Panopa zinthu zikuyenda kwambiri. Nyimbo zanga zambiri ndimagulitsa kudzera pamakinawa ndipo ndimayesetsa kuti nyimbo iliyonse yomwe ndatulutsa izifika pamakinawa ndipo kuteroko nyimbo zanga zimatchuka kwambiri msanga. n

Malamulo Khumi pa Wenela

 

Related Articles

Back to top button