Chichewa

Pimani onyamula mafuta

Listen to this article

Kati deru kadaopsa mlenje. Anthu okhala kwa Sonda komwe kuli nkhokwe za mafuta m’zinda wa Mzuzu sakumwa madzi ndi madalaivala amene amadzatula mafuta kuchokera m’dziko la Tanzania.

Pomwe tinkasindikiza nkhanyiyi n’kuti m’dziko la Tanzania anthu 285 akudwala matenda a Covid-19, 11 atachira ndipo 10 atamwalira ndi matendawa.

Izi zikupereka mantha kwa anthu a kwa Sonda kuti madalaivala omwe akubweretsa mafuta m’derali atha kuwatengera imfa.

Madalaivalawa akamalowa m’dziko muno sakuwabindikiza monga zikuyenera kukhalira pamene ukutuluka kapena kulowa m’dziko muno.

Galimoto zonyamula mafuta kungofika kumene kuchokera ku Tanzania

Koma mneneri wa unduna wa zaumoyo Joshua Malango adati anthu asachite mantha chifukwa boma liyamba kubindikiza madalaivalawo kwa sabata ziwiri pachipata cha dziko lino kuyambira sabata ino. 

Iye adati kusunga madalaivalawo kuthandiza kuthana ndi matendawo.

“Anthuwo sadziyezedwa ngati ali ndi Covid-19 kapena ayi mokakamizidwa, koma chizichitika n’chakuti aliyense wolowa m’dziko muno adzikhala kaye kwa sabata ziwiri pa malo olowerawa, kuti tione ngati akuonetsa zizindikiro za nthendayo ndipo aziyesedwa akaonetsa zizindikirozo,” adatero Malango.

Malinga ndi wapampando wa nthambi ya chitetezo m’deralo, Isaac Soko, madalaivalawo akafika kumeneko amakonda kuyendayenda, zomwe zikupereka chiwopsezo kuti atha kubweretsa mliri wa Covid-19 kuderalo.

Soko adati nthawi zina madalaivalawo amakhala oposa 40 koma satsatira ndondomeko zoyenera kuti asafalitse kapena kutenga matendawo.

“Tili pachiwopsezo chachikulu cha nthenda ya Covid-19 chifukwa anthuwa akuchokera m’dziko la Tanzania komwe nthendayi yafala kwambiri,” adatero Soko.

Iye adati mantha awo akuchuluka chifukwa madalaivalawo akafika m’dziko muno akumayendayenda ndi anthu a m’deralo.

Iye adati madalaivala ambiri ndi a chi Swahili ndiye akafika kuno Chichewa chimawavuto, zomwe zimawachititsa kuti atengane ndi Amalawi amene amalankhula Chichewa.

Mfumu ya deralo, Belewa, yomwe idadandaula za vutolo pamaliro mkati mwa sabatayi, idapempha boma kuti lidzionetsetsa kuti madalaivalawo akuyezedwa asadalowe m’dziko muno, komanso adzikhala ku mbindikiro wa sabata ziwiri.

Malo oyezera nthendayo m’chigawo cha kumpoto adatsekulidwa Loweruka pa April 11 ndipo pofika pomwe timalemba nkhaniyi anthu osapitilira khumi ndiwo adayezedwa.

Pa anthuwo, palibe adapezeka ndi nthendayo m’chigawocho.

Mneneri wa bungwe la National Oil Company of Malawi (Nocma), lomwe limabweretsa mafutawo, Telephorous Chigwenembe, adakana kulankhulapo pa zomwe akuchita madalaivalawo akafika m’dziko muno.

Dziko la Malawi nalo lili pa nkhondo yolimbana ndi matendawo. Pofika dzulo, anthu 33 ndi omwe adatsimikizika kuti akudwala matendawo, atatu adamwalira ndipo atatu ena adachira, kutanthauza kuti 27 ndi omwe akudwala matendawa. 

Maiko a Uganda ndi Kenya ndi ena mwa maiko omwe akudadandaula ndi madalaivala a galimoto zonyamula katundu. Mwachitsanzo, m’dziko la Uganda, madalaivala awiri ochokera ku Tanzania apezeka ndi nthendayo Lachitatu m’sabatayi.

Related Articles

Back to top button
Translate »