Chichewa

Pulofeti Meja wagawa dziko pawiri

Listen to this article

Mudamvapo inu zakuti ambiri amadana ndi mneneri kwawo komwe. Izi zikupherezera masiku omaliza ngati ano.

Abale anzanga, zidaliko pa Wenela tsiku limenelo pomwe adafika woimba wina, akuti David. Nyimbo yake idali yachilendo ndithu, ati Osaopa ya David kunyoza mkulu wina wotchedwa Meja.

Gawo lina la nyimboyo, imene ena atulutsa Part 2 akuti Rebirth ikumadutsa motere:

Ndikumva ziwanda zako zikuti

Eeh! Papa game yalakwa papa

Ufiti

Ndikupukusa legeni yanga kumwala

Ndine mwana wa Mulungu sungandiphe ndi mankhwala

tadeyo

Ukamaimvera nyimboyi, ikumamveka ngati ukuona uja Davide wa m’buku lopatulika, inde uja adapha chiphona Goliyati ndi mwala, yemwenso adapha mkango umene unkafuna kudya nkhosa zomwe amaweta!

“Uyu mneneri Meja ndithu wagawanitsa anthu pano pa Wenela. Aliyense lero akukhala wodana naye kapena womukonda. Amene akuchuluka sitikudziwa. Chomwe ndikudziwa nchakuti mneneriyu ulusi amauswa,” adatero Abiti Patuma.

“Kalekale ndinkakonda kuwerenga za Emmanuel N uja wa sataniki amene adalapa machimo ake. Iye ankakamba za ndalama, zovala, akazi okongola ndi zina zotero zochokera pansi pa madzi,” adatero Gervazzio, uku akuika nyimbo ya Piksy yatsopano ya Angozo.

“Nsanje idakula zedi pano pa Wenela. Ukalemera, ati sataniki. Ukakalamba, ati ufiti. Ukachita bwino ati walowa kashigeti. Uyu mneneri Meja mpatali. Go deep, real deep, mama,” adatero Abiti Patuma.

Mawu ake ali mkamwa adatulukira mneneri Meja. Adali atagwirira mmwamba, miyendo ili lende.

“Madzi ndi mpweya chopepuka n’chiyani? Kodi iye amene akuyenda pamadzi ndi amene akuyenda mumpweya, shasha ndi uti?” adafunsa mneneri Meja, mbale wa mneneri Bashir.

“Mneneri, kodi uneneri uli ngati matenda a pamphasa?” adafunsa Abiti Patuma.

Koma Abiti Patuma amadziwa kuphinduka ngati nyengo. Wasintha kale?

“Matenda a pamphasa, ndiye ati? Tell me more before the seed you plant bears you some miraculous bucks,” adatero Mneneri Meja, inde mbale wa mneneri Bashir.

“Matenda opatsirana pogonana. Uneneritu masiku ano uli ngati matenda a pamphasa: chindoko, chinzonono, mabomu ndi zina zotero. Ngati mwamuna awatenga, naye mkazi amugwira,” adayankha Abiti Patuma.

Ziii wakeyo!

“Nanga taonani mneneri mayi Meja adati wina adapemphera ndipo adapeza mwayi wa katapira. Koma kuti akabweze ndalama kwa mwini banki ya ku Chinayo, adamuuza kuti ayi, kulibe ngongole. Miraculous bucks imeneyo. Bwanji mukunamiza mtundu wanga?” adafunsa Abiti Patuma.

“Sindikuona chachilendo. Kalelo aneneri ngati ine tinkalasidwa miyala mpaka kufa. Mwaiwala Sitefano? Ndine Meja Sitefano,” adayankha munthu wa Mulungu.

Kukamba za Moya Pete! Mkuluyu wanyangala. Pajatu iyi ndi sabata imene Mfumu Mose idapita kumtsinje kukazula chinangwa. Ena amati mfumuyo idalowera kumtsinjeko pa 5 April, ena 6 enanso 7.

Moya Pete wakwiya zedi, ndipo pano wasuntha Mowe Pati kuti akhalenso otsutsa zonena za inu ndi ine. Mwamukumbuka mayi wathu muja adanenera kuti anthu a ku China atibwezere agalu ndi njoka zomwe ankadya pano pa Wenela? Ndiye mwamukumbuka mkulu uja Chiponda kaya Paponda? Pano akuti ndiye athane ndi njala. Uyutu ndi mkulu amene adati zotsitsa mpweya pano pa Wenela ayi!

Zikumveka kuti uyu ndiye mkulu alandire ndodo ya ukalamba ya Moya Pete!

Gwira bango mwaiwe. Madzi akutenga!!n

Related Articles

Back to top button
Translate »