Ruo asokoneza za uchembere wabwino

Listen to this article

 

Adali madzulo a pa 12 March 2015 pamene matenda a mayi Madalitso Ofeni, wa zaka 35, adakula. Nthawi ili cha m’ma 5 koloko adauyamba wa kuchipatala cha Trinity Mission ku Fatima m’boma la Nsanje, koma zidathina panjira. Nanga akadati mayi wotopayu?

Mothandizidwa ndi agogo ake omwe adamuperekeza, adangobisala kuseli kwa mlaza mmphepete mwa msewu ndipo movutikira koma mwamwayi, adabereka mwana wamkazi. Apo n’kuti nthawi ili cha m’ma 8 madzulo.

Demand for children should be reduced
Demand for children should be reduced

Amayi ena oyembekezera sakhala ndi mwayi woterewu—amatha kupita padera, ena kumwalira kumene pobereka chifukwa chosowa chithandizo ndi upangiri wa akuchipatala.

Nkhani zotere ndizo zatenga malo kwa Osiyana m’bomalo. Ukutu ndi komwe boma lidasamutsira ena mwa anthu okhudzidwa ndi ngozi ya kusefukira kwa madzi kuchigwa cha mtsinje wa Shire.

Kuchoka kuderalo kufika pachipatala cha Trinity pali makilomita 15 koma anthu odwala amayenda wapansi kaamba kosowa galimoto. Ambiri sayerekenza n’komwe chifukwa chipatalacho si chaulere.

Mkulu wa chipatalachi, William Allan, akuti mtengo wobereketsa mwana ndi K3 600 ndipo mtengowu umakwera malinga ndi momwe mwanayo wabadwira.

“Ikakhala opareshoni, mtengo umakwera kufika pa K15 000 mwina kuposera apa,” adatero Allan.

Chipatala chomwe chawayandikira ndi cha Makhanga chomwe chili pamtunda wa makilota 9. Anthuwa akhala akugwiritsa ntchito chipatalachi ngoziyo isadachitike, koma tsopano sangapitekonso chifukwa mtsinje wa Ruo wadutsa pakati ndipo palibe mlatho.

Ambiri amene ali kumalo atsopanowa katundu wawo adakokoloka ndi madzi ndipo boma pano lidasiya kuwapatsa chithandizo cha zakudya ndi zina zofunikira pamoyo wawo.

Ngati apeza ndalama chomwe akuyenera kuchita ndi kukagula chimanga chomwe pano chafika pa K8 600 pathumba la 50 kilogalamu kapena mpunga womwe ndi K10 000 pathumba losapuntha pamsika wa Fatima.

Gulupu Manyowa, yemwe wafungatira anthuwa, akuti ambiri mwa iwo sangakwanitse kupeza ndalamazi.

“Amene akupita kuchipatalako ndi ochepa,” idatero mfumuyi. Dera lake lili ndi midzi 11 ndi anthu 9 973.

Manyowa adati mwezi wa August wokha, amayi 20 ochokera midzi yomwe ili pansi pa ulamuliro wake aberekera pakhomo ndi chithandizo cha azamba.

“Amayi oposa 7 aberekera panjira akupita kuchipatalako. Vuto ndi loti sangapite kuti akadikirire komweko chifukwa nayo ndalama imakhala yokwera. Ndiye amadikirira kunyumba kuti anyamutse tsiku lomwe ayamba kudwala kuti akangofikira kubereka kuchipatalako,” adatero Manyowa.

Mzamba yemwe adakana kutchulidwa dzina poopa milandu, adati amayi oyembekezerawo akumawathandiza chifukwa akumakhala atopa kale ndipo sangayende kupita kuchipatala.

Mu 2007, boma lidaletsa azamba kuchiritsa amayi oyembekezera ndipo mmalo mwake lidati azingolimbikitsa amayi oyembekezera kupita kuchipatala.

Nduna ya zaumoyo, Dr. Peter Kumpalume, watsimikiza za mavutowa ndipo wati boma likuganiza zowamangira chipatala.

“Ndafufuzadi ndipo ndapeza kuti anthuwa alibe chipatala m’dera lawo. Poyamba timagwiritsira ntchito ma mobile clinic (zipatala zoyendayenda) koma pano [galimoto] zonse zidaonongeka. Yankho labwino n’kuti anthuwa tiwapatse permanent solution [yankho lokhazikika] komwe ndi kuwamangira chipatala.”

Titawafunsa kuti kodi   chipatalachi chimangidwa liti, ndunayi idati:

“Ndifufuze ndi a dipatimenti ya za mapulani (Planning Pepartment) pankhani yowamangira chipatalayo.”

Pali mantha kuti zomwe adaona Ofeni ndi amayi ena oyembekezera m’derali zingapitirire ngati sipakhala yankho lachangu kuti akhale ndi chipatala chawo.

Loweruka pa 12 September, Tamvani itayendera chipatalachi idapeza kuti mbali yomwe kumafikira amayi oyembekezera ochokera kwa Osiyana kudali mayi mmodzi yekha.

Mayiyu, Mboyi Filipi, wa m’mudzi mwa Tchereni adati amayi ambiri akuopa kulipira.

“Achimwene ndiwo andithandiza ndi ndalama zobwerera kuno. Amayi anzanga sakufika kuno chifukwa chosowa ndalama, komanso ndi kutali,” adatero Filipi.

Naye Fatinesi Fred, 54, wa m’mudzi mwa Manyowa adati sangapite kuchipatalako chifukwa alibe ndalama.

Fred tidamupeza ndi mwana wake amene adatuluka nsungu thupi lonse. Akumangomukumbira mankhwala azitsamba.

“Sabata ino ndi yachiwiri mwanayu akuvutika ndi nsungu. Kuti ndipite kuchipatala ndi vuto ngati limeneli ndiye kuti ndikuyenera kukhala ndi K1 200. Chakudya tilibe, tikugonera mango, nditapeza ndalama bola ndikagule chimanga kuti mwanayu adyeko,” adatero Fred.

Mneneri wa nthambi yoona za ngozi zogwa mwadzidzidzi ku Department of Disaster Management Affairs (Dodma), Jeremiah Mphande, adati madera ambiri amene adasamutsirako anthu okhudzidwa ndi ngozi za madzi osefulira akukumana ndi mavuto osiyanasiyana koma ntchito imeneyo si yawo.

“Mavuto alikodi, koma ntchito yathu idali yopulumutsa anthuwa ndipo zina n’zokudza maundunda ena,” adatero Mphande.

Related Articles

Back to top button