Chichewa

Sandulizani tomato, iphani makwacha

Listen to this article

Pamene m’nyengoyi tomato amatsika mtengo chifukwa cha kuchuluka pamsika, katswiri pa luso lopanga zakudya zosiyanasiyana kuchokera ku mbewu za zipatso ndi masamba akuti anthu akhonza kumusanduliza ndikumapha naye makwacha.

Katswiriyu, Kingsley Masamba wa kunthambi yoona za luso la makono la zakudya ku Lilongwe University of Agriculture and Natural Resources (Luanar) adafotokoza kuti zakudya zopangidwa kuchokera ku mbewuyi zimakhala za mtengo wokwera choncho anthu akhonza kuchitirapo mwayi.

Iye adaonjeza kuti kumukonza tomato m’njira yoti akhalitse kwa nthawi yaitali n’kumadzagulitsa m’nyengo imene amakwera mtengo ndi msampha wina wokolera ndalama.

Nthawi yotentha tomato amakhala ali mbweee!

“Vuto ndi loti kwathu kuno timangodziwa kulima koma kuti tisinthe maganizo ndikuyamba kukonza mbewu ndi kumagwiritsa ntchito zimavuta n’chifukwa chake zimakhala zotsika mtengo ndi zosowa misika ndi kumangoongeka.

“Tomato sauce ndi tomato paste timagula m’sitolo za m’dziko muno wochokera kunja amapangira tomato amene timalimayu,” iye adatero.

Masamba adaonjeza kuti kuonjezera pa tomato sauce ndi tomato paste anthu akhonza kupanga tomato wa ufa, jamu wopaka pa buledi ngakhalenso juwisi.

Iye adatsindika kuti zinthuzi ndi zosavuta kupanga ndipo sizilira zambiri choncho ngakhale pakhomo anthu akhonza kumapanga ndi kumazigwiritsa ntchito kapena kuyamba ngati bizinesi.

“Vuto limene limakhalapo mwachitsanzo popanga tomato waufa ndi loti amafuna dzuwa lochuluka choncho ndi zokomera m’madera motentha monga ku chigwa cha mtsinje wa Shire, Salima ndi madera ena a m’mphepete mwa nyanja,” adatero Masamba.

Goodwill Phiri wa m’boma la Lilongwe amapanga tomato waufa ndi kumagulitsa m’dziko muno ngakhale kunja.

Iye adati kufunika kwa dzuwa lokwanira pokonza tomatoyu kudamuchititsa kuti asamakonzere tomatoyu m’bomali chifukwa dzuwa limacheperapo.

Iye adaganiza zokaika fakitale yake ku Salima kuti azitha kuumitsa mosavuta.

“Ndidayamba izi m’boma la Lilongwe koma masiku ena dzuwa likabwera lochepa asadaume amaonongeka,” iye adatero.

Kuonjezera apo, Phiri adati kuumitsaku kumachitika bwino mu zipangizo zoumitsira kuti ufa wake uzikhala wa maonekedwe a pamwamba komanso michere ina isachokemo.

Iye adati poyamba asadapeze zipangizozi amangoyala pepala pa dzuwa ndi kuyanika tomato wake wodula bwino koma fumbi ndi ntchentche sizimakata pamalopo choncho ufa wake umaoneka wakuda.

“Chipangizochi dzina lake ndi “green house” yoyanikira tomato ndipo imaoneka ngati nyumba yapepala.

“Mkati mwake mumakhala thandala loyanikirapo choncho chifukwa cha kutentha kwambiri kwa m’nyumbamu sachedwa kuuma komanso chifukwa choti ndi mkati simulowa fumbi ndi ntchentche, ufa wake umakhala wooneka bwino kwambiri,” iye adatero.

Kopaletive ya Mwinama m’boma la Ntchitsi nayo imapanga jamu wa tomato.

Malingana ndi mmodzi mwa mamembala a gululi Ireen Golombe, kuonjezera pa tomato amagwiritsa ntchito shuga kuti azitsekemera bwino, sodium benzoate kuti azisungika kwa nthawi yaitali ndi citric acid kuti azimveka kakomedwe kopatsa mudyo.

“Poyamba timatsuka tomato wathu ndipo tikamaliza timamuika mogayira. Chogairachi chimatulutsa phala kwalokha komanso nthangala ndi makoko paokha pamapeto pake timaliphika ndi kuthira zoonjezerazo ndi kulongeza m’mabotolo,” adafotokoza motero.

Iye adati anthu okhala mozungulira deralo amamukonda jamuyi kwambiri koma ali ndi chilinganizo choti kutsogoloku apeze chiphaso kuti azigulitsa m’sitolo zikuluzikulu za m’mizinda ya m’dziko muno.

Related Articles

Back to top button