Chichewa

Sankhani Mkandawire kulavula moto

Listen to this article

 

Sankhani ‘Mkango Plus’ Mkandawire adachoka ku Nyasa Big Bullets chaka chino kupita ku Tanzania komwe akusewera Mbeya FC. Iye adachoka limodzi ndi Owen Chaima ndipo ulendowo udali ndi zokamba zambiri. BOBBY KABANGO adacheza naye motere:

Mkandawire: Kumalankhulidwa zambiri

Tidziwe mbiri ya Sankhani…

Ndimachokera ku Dwangwa m’boma la Nkhotakota. Ndine wachisanu mwa ana 7. Ndine wosakwatira koma posakhalitsapa mumva nthungululu. Ena amanditchula Mkango Plus, dzinali adandipatsa ndi sapota wa Bullets ati chifukwa omwetsa zigoli amavutika akakumana nane. Ndidayamba kusewera Bullets mu 2007 kuchokera ku Dwangwa United. Ndaseweranso Carara Kicks ku South Africa.

Moyo uli bwanji ku Mbeya?

Zonse zili bwino, moyo ndi choncho, pena ziwawe pena kukoma koma ndili bwino. Ku Mbeya ndikusewera pafupifupi masewero alionse.

Kuchoka kwako ku Bullets padali zokamba zambiri, zidatere chifukwa chiyani?

[Waseka..] Bobby aliyense amanena choncho koma pamene ndimachoka ku Bullets n’kuti atagula [John] Lanjesi, [Emmanuel] Zoya komanso adali ndi [Miracle] Gabeya omwe akadagwira ntchito yanga. Kumbukiranso adali ndi George [Nyirenda]. Ndidaona kuti idali nthawi yabwino kusuntha chifukwa ndakhala ndi timuyi ilibe kanthu mpaka pamene ndimachoka itapeza ndalama.

Umawathawa anzakowa?

Ayinso, koma kuona moyo wanga komanso kutimuko kumalankhulidwa zambiri zomwe zikadasokoneza tsogolo langa ndiye ndidafuna ndisunthe kuti ndikaone zina.

Tinene kuti tcheya wakale Sam Chilunga ndiye adapangitsa?

[Waseka…] Amene uja adali ndi masomphenya, sindingakuuzeni zambiri koma taganizani poyamba ndimalandira K33 000 ngati malipiro anga a pamwezi. Anthu amatamanda za luso langa koma kumaposedwa ndalama ndi wonenerera basi, zoona izi? Munthu uja adakweza malipiro ndiye padalakwika?

Umadandaula kuti Chilunga adachotsedwa?

Ndizomvetsa chisoni kumene, tinene chilungamo Chilunga adali kamuna. Adapeza ma sponsor, adakweza ndalama yolandira tikasewera gemu komanso simungamumve Chilunga akulankhula m’manyuzipepala kupempha thandizo.

Kodi ukudana ndi mtsogoleri wapanoyu Noel Lipipa?

Sindikuteronso, koma Lipipa adziwe kuti akuyenera kukhala wa mphamvu chifukwa [Bullets] imakhala yosiirana. Aonetsetse kuti osewera akusangalala ndipo zikatere amupatsa zomwe akufuna, dzina lake litchulidwa paliponse chifukwa Chilunga amaganizira osewera kwambiri.

Mawu ako ku Bullets ndi wotani?

Tiyeni tipemphere kuti Kamuzu Barracks ipunthwe ndipo ife tipambane magemu atsala kuti titenge ligi. Ine ndi wa Maule ndipo kubwera kumudziko timu yanga ndi imeneyi. n

Related Articles

Back to top button
Translate »