Nkhani

Shuga apezeka posachedwa—Illovo

Mkulu wa kampani yopanga shuga ya Illovo Malawi Mark Bainbridge wati kampaniyo iyesetsa kuti shuga azipezeka chaka chonse osati kumasowa momwe zakhalira sabata zingapo zapitazi.

Bainbridge adanena izi Lachitatu pomwe nduna ya zokopa alendo ndi malonda Joseph Mwanamvekha adayendera kampaniyo kuti akamvetsetse za gwero la kusowa kwa shugayo. Kusowa kwa shuga kudachititsa kuti ogulitsa akweze kuchoka pa K750 kufika pakati pa K950 ndi K1 200.

Ogwira ntchito ku Illovo pakalikiliki kupanga shuga

Malinga ndi Bainbridge, chaka chino kampaniyo inagulitsa shuga olemera matani 244 000, pomwe dziko lino limalira matani 160 000 ndipo anadabwa kuti shugayo akusowa bwanji.

“Tinali ndi shuga wokwanira chaka chino ngakhale mvula siyinagwe bwino nthawi yomwe timabzala nzimbe. Ogulitsa ena amagula shuga wochuluka n’kumusunga zomwe zimadzetsa mavuto ngati awa,” adatero iye.

Iye adati padakalipano, kampaniyo ikuyesetsa kuti iwonjezere shuga amene imapanga kuti azikwanira chaka chonse.

Mwanamvekha adati ndi wokondwa chifukwa kampaniyo yalonjeza kuti izipanga matani 650 a shuga patsiku, pomwe dziko lino limalira matani 411 patsiku.

“Tazindikira kuti pali shuga wochepa pamsika, zimene zachititsa kuti mtengo ukwere. Kwa amene akukweza shuga mopweteka Amalawi, malamulo agwirapo ntchito. Tili ndi chiyembekezo kuti Illovo ikwaniritsa lonjezo lake kuti shuga ayambe kupezeka,” adatero Mwanamvekha.

Pomwe Amalawi akudikira shugayo kuti ayambe kupezeka, Amalawi amene tidacheza nawo anadandaula ndi kusowa kwa shugako, ponena kuti izi zikuchititsa moyo kuthina.

Mmodzi mwa Amalawiwo, Joana Chimphamba wa kwa Senti ku Lilongwe, adati abizinesi ena kumeneko akumaphwatula paketi ya kilogalamu imodzi ndi kuigawa pawiri. Gawo lililonse akuligulitsa K600 kapena K650.

“Izi zikutanthauza kuti yomwe timagula K780 pa paketi tikugula K1 200 kapena K1 250. Nanga akapitirira kusowa shugayu, zitithera bwanji?” adadabwa  iye.

Chimvano Moyo wa ku Area 25 wati poyamba sadakhulupilire atatuma mwana kukagula shuga Lamulungu lapitali ndipo pobwera adamuuza kuti adagula pa mtengo wa K970 chikhalirecho, amagula pamtengo wa K780.

Iye wati atapita kukatsimikiza kumsika, adapeza kuti magolosale ambiri alibe shuga ndipo pomwe adamupezapo adamutsimikizira kuti shuga akusowa ndipo akapezeka akukhala okwera mtengo.

Mmodzi mwa anyamata ogwira ntchito mushopu yaikulu ya Spar mumzinda wa Lilongwe adati patenga nthawi shopuyi isanalandire shuga kuchokera ku Illovo.

Iye adati anthu ambiri akhala akubwerera mushopuyi akafuna shugayo ngakhale kuti eni ake adapereka kale oda ya katunduyu koma sadanene kuti shugayo samabwera chifukwa chiyani.

Ndipo mumzinda wa Blantyre, anthu ochuluka amakhamukira kusitolo zosiyanasiyana monga Shoprite kumene kumakhala miyandamiyanda ya anthu pamzere kufuna kugula shuga akapezeka.

Davie Chilikumwendo wa ku Namiyango mu mzinda wa Blantyre adati wasiya kumwa tiyi chifukwa ndalama ya shuga siyikukwanira.

“Shuga yemwe akupezeka akugulitsidwa pamtengo wokwera. Padakalipano tizigwiritsa mchere m’phala ndipo tiyi adzamwedwa shuga akayamba kugulitsidwa pa mtengo woyenera,” adatero Chilikumwendo.

Nawo ochita malonda mumzindawu ati kusowa kwa shuga kukusokoneza bizinezi chifukwa amadalira yemweyi popanga phindu lochuluka. Mmodzi mwa iwo, Clement Chafoteza wa ku Chilobwe, adati shuga wochepa yemwe akupezeka akugulidwa modula ndipo anthu wamba akukanika kuagula.

“Chuma chikusokonekera chifukwa bizinezi yanga imadalira shuga. Phindu lochuluka limachitika shuga akamapezeka chifukwa anthu amagula pamtengo woyenera,” adatero Chafoteza. n

Related Articles

Back to top button