Nkhani

Si zonyengerera mu 2016—Mkulu wa polisi

Listen to this article

Anthu ali kalikiriki kukonza mapulani a chaka chatsopano cha 2016 koma ngati mapulani ake akukhudza umbanda ndi ziphuphu, dziko lake si lino, waneneratu mkulu wa Polisi m’dziko muno, Lexten Kachama.

Kachama adalankhula izi pa 31 December 2015 pomwe apolisi amakondwerera chaka chatsopano kulikulu la polisi ku Area 30 mumzinda wa Lilongwe.

Lexten Kachama
Lexten Kachama

“Chaka cha 2016 chikhala chaka cha chitsanzo pankhani yolimbana ndi mchitidwe wa uchifwamba, umbanda ndi ziphuphu. Tithana ndi zigawenga zonse komanso onse omwe akufuna kulemera kudzera m’ziphuphu,” adatero Kachama.

Iye adati m’chaka cha 2015, apolisi adayesetsa kulimbana ndi mchitidwe wa uchigawenga ndi umbanda koma ngozi za pamsewu zidakwera ndi 18 pangozi 100 zilizonse kuyerekeza ndi m’chaka cha 2014.

Kachama adati chimodzi mwa zifukwa zomwe zidachititsa izi ndi ziphuphu zomwe apolisi ena apamsewu amalandira kuchokera kwa eni galimoto zosayenera kuyenda pamsewu.

“Nkhani ya ziphuphu ndi imodzi mwa nkhani zomwe apolisi amatchuka nazo makamaka pamsewu. Komabe ndinene pano kuti si apolisi onse omwe amachita izi koma apolisi ochepa chabe adyera,” adatero Kachama.

Iye adati chaka chino akhwimitsa chilango chomwe apolisi opezeka ndi mlandu wa ziphuphu amalandira ndipo adachenjezanso anthu omwe amakopa dala apolisi ndi ndalama kapena zinthu zina kuti awatsekere milandu yawo.

Malinga ndi kafukufuku wathu, wapolisi wongolembedwa kumene ntchito, maka amene ali ndi satifiketi ya fomu 4, amalandira ndalama zosaposera K50 000 asanaduleko msonkho.

Ndi mmene mitengo ya zinthu ilili panopa, n’kosatheka kuti munthu akwaniritse zofunika pamoyo wake wa tsiku ndi tsiku ndi malipiro achepa ngati awa poganizira chakudya, nyumba ya lendi, fizi ya ana asukulu, zovala ndi zina zotero zofunika pamoyo wa munthu.

Mwina ichi n’kukhala chimodzi mwa zifukwa zomwe mchitidwe wa katangale ndi ziphuphu watenga malo pakati pa apolisi.

Kachama adalonjeza kuti apolisi ayesetsa kugwira ntchito yokomera anthu koma adati kuti izi zitheke, anthu akuyenera kutengapo gawo makamaka potenga apolisi ngati abwenzi awo powatsina khutu akawona

zodabwitsa mmadera momwe akukhala.

Pothirapo ndemanga, mkulu wa bungwe loona za maufulu a anthu la Centre for Human Rights and Rehabilitation (CHRR), Timothy Mtambo, adati uthenga wa mkulu wa polisiyu wafika panthawi yoyenera pomwe malingaliro a zauchifwamba za mu 2015 akadali m’mitima.

Iye adati m’chaka changothachi, uchifwamba udakula mpaka apolisi kumaphedwa ndi zigawenga zomwe zimadetsa anthu nkhawa pazachitetezo cha moyo ndi katundu wawo.

“Chitetezo ndiye gwero la chitukuko cha mtundu uliwonse. Mabizinesi, zipembedzo, ufulu wa anthu ngakhaleso zomangamanga zimayenda bwino pakakhala chitetezo chokwanira chifukwa anthu amapanga zinthu mtima uli mmalo,” adatero Mtambo.

Iye adati pulani ya apolisiyi singatheke pokhapokha boma litaikapo mtima powapatsa zipangizo zokwanira zogwirira ntchito yawo komanso kuwaganizira pankhani ya umoyo ndi makhalidwe awo.

Mwa zina, Mtambo adati apolisi amasowa chilimbikitso kaamba kakuti malipiro omwe amalandira ndi ogwetsa mphwayi, zomwe zimawafoola nkhongono; nyumba zomwe amakhalamo n’zosaoneka bwino; komanso amagwira ntchito popanda zodzitetezera.

“Nthawi zina apolisi amalephera kupita kukagwira ntchito yawo kaamba kosowa mayendedwe chifukwa cha nkhani za mafuta komanso galimoto. Apolisi amapezeka kuti akugwira ntchito mmalo a zipolowe koma alibe zodzitetezera, choncho sangagwire ntchito momwe akadagwirira chifukwa nawo ndi anthu, amafuna kudziteteza,” adatero Mtambo.

Related Articles

Back to top button
Translate »