Nkhani

Sindidalakwe, watero Wandale

Listen to this article

 

Mtsogoleri wa gulu lomenyera ufulu wolanda malo m’maboma a Thyolo ndi Mulanje la People’s Land Organization (PLO) Vincent Wandale, yemwe bwalo la milandu la Blantyre Magistrate lidampeza wolakwa pamilandu itatu ndi kumugamula kuti akhale miyezi 18 asadapalamulenso, wati iye sadalakwe ndipo achita apilo kubwalo la milandu lalikulu.

Wandale, yemwe pa 1 September  chaka chino adamemeza anthu kukalowerera esiteti ya tiyi ya Conforzi m’boma la Thyolo ati ponena kuti malowo ndi a makolo awo, adapezeka wolakwa pamilandu yolowerera malo a eni popanda chilolezo komanso kupanga upo woipa.wandale

Ndipo Lachiwiri lapitali , Wandaleyu adagamulidwa ndi woweruza milandu wamkulu pabwalo la milandu la Blantyre, Thokozani Soko.

Polankhula ndi Msangulutso Lachinayi lapitali, Wandale adati sadakhutire ndi chigamulocho chifukwa padali zolakwika zingapo.

“Ine ndikukhulupirira kuti sindidalakwe ndipo pachifukwa ichi, ndikasuma kuti bwalo lalikulu liunikenso chigamulo chomwe adandipatsa. Pali zinthu zina zingapo zomwe sadaziyang’anitsitse poweruzapo ndipo ndikukhulupirira kuti bwalo lalikulu likaziunika zimenezi,” adatero Wandale.

Iye adati mwachitsanso, bwaloli silidampeze kuti upo omwe adapangitsa udali utiuti ndipo ankatani. Iye adati izi zidalibe umboni weniweni.

Ndipo chachiwiri iye adati abwaloli sadapenzenso umboni kuti iye adapita nawo kuesiteti ya Conforzi ati kaamba koti iyeyo kudalibe kumaloko patsikulo.

“Chachitatu ndi choti ifetu anthuwa tidawalembera kalata kuwadziwitsa za dongosolo lathu, koma iwowa sadayankhe zomwe kwa ife tidatanthauzira kuti ativomereza kukalowa kumalowa. Sitikumvetsa chifukwa chomwe abwalo akunenera kuti tidaphwanya lamulo pomwe anthu tidawadziwitsa bwino lomwe,” adalongosola motero.

“Ndikukhulupirira kuti sangakandilowetsenso jere chifukwa mlanduwu ngwaung’ono komanso palibe adagwiritsa ntchito malo a Conforzi komanso nkhaniyi ndi ya gulu,” adatero Wandale.

Polankhulapo, mlembi wa bungwe loona za malamulo m’dziko muno la Malawi Law Society (MLS), Khumbo Soko, adati Wandale ngati munthu wina aliyense ali ndi ufulu wokasuma ngati sadakhutitsidwe ndi chigamulo.

“Ngakhaletu sali kundende, koma sikuti Wandaleyu ndi mfulu ayi, choncho ali ndi ufulu wokasuma,” adatero Soko.n

Related Articles

Back to top button