Nkhani

Sipakala waimitsa Nyumba ya Malamulo

Listen to this article

Sipikala waimitsa Nyumba ya Malamulo kwa sabata ziwiri kaamba ka phungu ndi ogwira ntchito ena ku nyumbayi omwe akhudzidwa ndi matenda a Covid-19.

Sipikala Catherine Gotani Hara wati akatswiri akhala akupopera mankhwala ndi cholinga chokupha tizilombo toyambitsa Covid-19 panthawi yomwe nyumbayi ikhale yotseka.

Akufuna kupulumutsa anthu: Gotani Hara

“Tapanga izi pofuna kuteteza aphungu ndi ogwira ntchito ku Nyumba ya Malamulo chifukwa aphungu ndi ogwira ntchito ena apezekako ndi Coronavirus ndiye zatipatsa mantha,” adatero Gotani Hara.

Malipoti ochokera ku unduna wa zaumoyo akusonyeza kuti aphungu ena apezeka ndi Covid-19 ndipo akulandira chithandizo.

Izi zidayamba kumveka sabata ziwiri zapitazo chitsirizireni mkumano wa aphungu womwe udavomereza bajeti yoposa K722 biliyoni yongoyembekezera ya miyezi inayi.

Pamkumanowo, Nyumba ya Malamulo idakhazikitsa ndondomeko zopewera kufala kwa Covid-19 zomwe mwa zina zidali kuchepetsa chiwerengero cha aphungu okhala m’nyumbayo pa nthawi yokumana, kuchepetsa maola okumana, komanso kuika zipangizo zosambira m’manja m’malo osiyanasiyana.

Pachifukwa ichi, alendo samaloledwe kukaonera zokambirana za nyumbayo.

Kadaulo wa zaumoyo George Jobe adayamikira utsogoleri wa nyumbayo pokhazikitsa ndondomekozo panthawi yomwe boma lidali pakalikiliki kuphunzitsa anthu njira zopewera Covid-19.

“Nyumba ya Malamulo yaonetsa chitsanzo chabwino chifukwa anthu amamvetsetsa ngati wolankhulayo akuonetsa chitsanzo chabwino,” adatero Jobe.

M’modzi mwa apampando a komiti yolimbana ndi Covid-19 John Phuka adati dziko la Malawi likuyenera kutsatira ndondomeko zones zothandiza kuchepetsa kufala kwa matendawa.

“Tikuyenera kupanga zotheka zonse kuti kachilombo kameneka kasapitirire kufala m’dziko muno.

“Pali njira zina zomwe tikutsatira kale monga kusamba m’manja, kuvala zotchingira kunkhope, kupewa malo wothinana komanso kupewa kupatsana moni wam’manja,” adatero Phuka.

Dziko la Malawi lidapeza anthu atatu oyambirira omwe anali ndi Covid-19 pa April 3 2020, koma pofika pa July 15 2020 chiwerengero chidali chitafika pa 2 614.

Mwa anthu omwe adapezeka ndi Covid-19, anthu 1 566 akadadwala, anthu 1 005 adachira ndipo anthu 43 adamwalira. Mwa anthu omwe adamwalira, 35 ndi amuna pamene 8 ndi amayi.

Malingana ndi komiti yolimbana ndi Covid-19, abambo ambiri ndiwo akupezeka ndi matendawa poyerekeza ndi amayi.

Related Articles

Back to top button