Nkhani

Siteshoni ya Nkaya ifewetsa maulendo

Gawo lachiwiri lomanga siteshoni ya sitima ya Nkaya m’boma la Balaka layamba ndipo ntchitoyi ikuyembekezeka kutha mu November chaka chino.

Mneneri wa bungwe loona sitima zapamtunda la Central East African Railways (CEAR) Chisomo Mwamadi wati gawoli likatha, anthu amene amagwiritsira ntchito sitima zapamtunda athandizika chifukwa sitima zizinyamula katundu wambiri komanso ziziyenda mwachangu.

Mwamadi: Samalani njanji
Mwamadi: Samalani njanji

Mu June chaka chino, bungweli lidamaliza gawo loyamba lomwe kudali kumanga njanji zinayi kuti sitima zapamtunda zizidutsana pamalopa.

Gawo lachiwiri lidayamba litangotha gawo loyamba lomwe kukhale kumanga njanji ina yotalika ndi makilomita awiri komanso kumanga njanji zinayi zomwe zizithandiza kusungirako sitima komanso kumasula mabogi.

“Njanji zimenezi ndizomwe tizimasulira sitima ngati ili ndi vuto komanso kusungirako sitima. Pamene tikupanga izi, sitima zina zizitha kumayenda mopanda kusokonezedwa. Izi sizimachitika poyamba chifukwa tidalibe malo, koma tsopano izi ziyamba kuchitika popanda vuto lililonse,” adatero Mwamadi.

Padakali pano, malo amene amangepo njanjizi asalazidwa kale komanso katundu wafika kuti ntchitoyi iyambe tsiku lililonse.

Njanji yopita ku Nkaya ndi imeneyi
Njanji yopita ku Nkaya ndi imeneyi

Mwamadi akuti gawoli likatha, anthu amene amagwiritsira ntchito sitima asangalala kwambiri komanso bizinesi izichitika mwachangu.

“Zonse zikatha, ndiye kuti Nkaya akhala malo akulu pomwe sitima zizisemphana komanso kumamangirira mabogi. Sitima yochokera ku Mwanza, Blantyre, Liwonde komanso Kanengo zizidutsana pa Nkaya komanso titha kumamanga mabogi.

“Izi sizimachitika poyamba. Kudutsana kwa sitima kudali kovuta, komanso sitimatha kumangirira mabogi. Poyamba ntchitoyi imachitikira ku Liwonde koma malo adali ochepa. Pofika November chilichonse chikhala chikuchitika, sitima ziziyenda mwachangu, zizinyamula mabogi ambiri, kuchoka pa 20 kufika pa 45. Anthu ogwiritsira sitima ayembekezere chimwemwe,” adatero Mwamadi. n

Related Articles

Back to top button