Nkhani

Siyayo Mkandawire atisiya

Listen to this article

 

Thambo lagwa kubanja la a Mkandawire a m’mudzi wa Zebera m’dera  la Mfumu Yaikulu M’mbwelwa m’boma la Mzimba komwe akulira imfa ya Siyayo Mkandawire, kholo lomwe akhala akulidalira muzonse.

Kadimba Mkandawire, yemwe ndi mmodzi mwa ana malmuyu, adati bambo awo adamwalira m’bandakucha wa Loweruka lathali atadwala nthawi yaitali.Photo of late Siyayo Mkandawire

Siyayo Mkandawire adatchuka kwambiri ndi gule wa vimbuza makamaka munthawi ya ulamuliro wa malemu Kamuzu Banda.

Ndipo ndi thandizo la Kamuzu Banda, Mkandawire adalembedwa ntchito m’boma komanso adayenda maiko ambiri kukasangalatsa anthu ndi mavinidwe ochititsa chidwi.

“Ndi zachisoni kwmbiri kuti tsopano tatseka mbiri ya madalawa pomwe taika thupi m’manda. Banja lathu lataya kholo lomwe limatithandiza muzambiri. Awa ndi madala omwe adatsalapo odziwa chikhalidwe chathu ndipo amayesetsa kutiphunzitsa tonse,” Kadimba adauza Tamvani kudzera pa lamya Lamulungu lapitali.

Koma mkuluyu adatsindika kuti izi sizikutanthauza kutha kwa gule wa vimbuza.

Kadimba adati iye ndi wokonzeka kupitiriza pomwe bambo awo adasiyira n’cholinga cholimbikitsa chikhalidwe chawo.

“Ndimathokoza kuti madala adandiphunzitsanso kuvina ndipo pano ndimavinanso kwabasi moti anthu sangasiyanitse ndi mmene ankavinira bambo anga. Ndipitiriza kutero n’cholinga choti ana anganso aphunzire,” iwo adatero.n

Related Articles

Back to top button
Translate »