Nkhani

Sukulu zitsegulidwanso

Listen to this article

Mkokemkoke umene udalipo pakati pa aphunzitsi ndi boma watha tsopano ndipo ophunzira amayenera kubwerera kusukulu dzulo Lachisanu.

Izi zadza kutsatira msonkhano wa atsogoleri a bungwe la aphunzitsi la Teachers Union of Malawi (TUM) ku Lilongwe Lachinayi nduna ya maphunziro Agnes NyaLonje atauza Nyumba ya Malamulo kuti komiti yoona za matenda a Covid 19 idati palibe ndalama za mswahala chifukwa aphunzitsi angakhale pachiopsezo chotenga matenda a Covid 19. M’sabatayi, atsogoleri a TUM adakumana ndi mtsogoleri wa dziko lino Lazarus Chakwera pankhaniyi.

Ndipo Lachinayi masana, wachiwiri kwa wotsatira pulezidenti wa TUM Rehema Harid adati bungwelo lidagwirizana zoti aphunzitsi abwerere kuntchito dzulo Lachisanu.

Iye adati adachita izi potsatira lamulo la Pulezidenti Chakwera kuti aphunzitsi onse ayambe ntchito yawo.

“Ngati bungwe, tikuyenera kutsatira zonena za Pulezidenti ndiye ngati wati tibwerere m’kalasi ife tingakane? Apapa aphunzitsi akubwerera m’kalasi mawa [dzulo],” adatero Harid.

Koma titafunsaso Pulezidenti wawo Willie Malimba adati iye sakugwirizana ndi zomwe adaulutsa achiwiri awowo.

Ophunzira m’sukulu za boma amayenera kuyamba sukulu Lolemba koma izi sizinatheke chifukwa aphunzitsi amanyanyala ntchito zawo pofuna kukakamiza boma kuti liwalipire mswahala wa chiopsezo chotenga matenda a Covid 19 akugwira ntchito.

Sukulu zimayenera kutsegulira Lolembalo mtsogoleri wa dziko lino Chakwera atanena kuti zitero patatha sabata zisanu zili zotsekedwa poopa kufala kwa matenda a Covid 19. Koma pofika Lachinayi maphunziro adali asadayambe.

Ndipo ngakhale Chakwera adakumana ndi bungwe la aphunzitsiwo palibe zidaphula kanthu. Nkhaniyo adaitula ku komiti yoona za matendawa yomwe idati palibe mswahala wotere.

Polankhula m’Nyumba ya Malamulo, nduna ya maphunziro NyaLonje adati komiti yotsogolera polimbana ndi matenda a Covid 19 yati palibe ndalamazo.

Iye adati: “Komitiyo yati aphunzitsi si ali m’gulu la oyenera kulandira mswahala wotere. Pali chitsimikizo choti aphunzitsi adzakhala m’gulu la anthu oyamba kulandira katemera othana ndi matendawa.”

Malimba mmbuyomu adati aphunzitsi adanyanyala ntchito chifukwa boma lidakana limodzi mwa mapempho awo atatu. Iye adati, boma lidavomereza kuonjezera malo ophunzirira ndi kulemba aphunzitsi oonjezera komanso kugula zodzitetezera.

“Sitilowa m’kalasi mpaka nkhani ya mswahara ataivomereza,” adatero Malimba.

Polankhula ndi mtolankhani wathu, kadaulo pa zamaphunziro Benedicto Kondowe adati mpungwepungwewu udadza kaamba ka chidodo cha boma chifukwa aphunzitsiwo adayamba kupempha mswaharawo chaka chatha.

“Koma kusamvana pakati pa TUM ndi boma kwazunzitsa ophunzira. Ena mwa iwo ndi asungwana omwe akutha misinkhu. Iwo amafunika kuthamanga ndi sukulu kuti akamatha msinkhu azikhala atazindikira kufunika kwa sukulu ndiye sakhala ndi maganizo a banja msanga,” adatero Kondowe.

M’masamba a mchezo mukuzungulira kanema wa msungwana wa sukulu ya pulaimale akunena mosapsatira kuti sukulu zikangotsekedwanso basi akupita kubanja.

“Ife asungwana timakula changu kuposa anyamata ndiye izi zoimaima sukuluzi tipezeka kuti takalambira pasukulu. Akangoyerekeza kutsekanso sukulu mwachibwana basi tingopita kubanja,” adatero msungwanayo.

Mlembi wamkulu muunduna wa zamaphunziro Kiswell Dakamau adati boma lalemba aphunzitsi ena 3 270 pofuna kuyankha nkhawa ya aphunzitsi yochepetsa chiwerengero cha ana omwe amayang’aniridwa ndi mphunzitsi mmodzi.

Mneneri kuundunawo Chikondi Chimala adati kupatula kulemba aphunzitsi ena, boma likumanga mabuloko a sukulu 383, lukukumba zitsime 640, kugula mabolodi ophunzitsira ochita kunyamula 5 000 komanso likugula makatoni 13 000 a sopo.

Koma Dakamau adati ngakhale pali zochitika zonsezi, aphunzitsi atemetsabe nkhwangwa pamwala.

“Tayesa kukamba ndi TUM kuti poti zina zonse mwa zofuna zawo zakonzedwa kupatula za mswahara abwerere m’kalasi uku tikukambirana mbali inayo koma ayi akuti sizingatheke,” adatero Dakamau.

Chaka chatha boma lidatsekaso sukulu kwa miyezi 5 ndipo chaka chino zatsekedwa sabata 5 kuchokera pomwe adangotsegulira telemu yoyamba pa 4 January.

Related Articles

Back to top button
Translate »