Chichewa

Tadeyo Mliyenda: Malingaliro padziko

Listen to this article

Ndidakhala pa Wenela kudya mpweya. Minibasi zoti ndiyitanire abale anzanga, osabwera n’komwe.
Ndidagwera m’maganizo. Ndidakumbukira zoti pali mkulu wina yemwe akufufuza maganizo a anthu pankhani ya bajeti. Nanga kodi njonda imeneyi pa Wenela ifika liti?
Ikadzangoti yafika, ndithu ndidzayiuziratu kuti pa Wenela patukuke. Tikufuna malo abwino ogona ife oyitanira; pakhalenso khitchini yoti tizikadya ulere; apolisi asamatiphwanyire ufulu wathu wopata chuma; komanso pakhale zimbudzi zoti tikalowa kukapuma, tisamalipire.
Abale anzanga, mzinda wonse wa Blantyre mulibe malo omwe munthu angayimirire mwaulele. Chonsecho akuti munthu ukagwidwa pamtengo, wakundende ndithu.
Nanga zinyalala pa Wenela, mkulu wachikwama athana nazo bwanji?
Ndikudziwatu mukundinena: A Tade, zoona chikwama chimanyamulidwa chija mukakhale zomanga zimbudzi pa Wenela? Simukudziwa chomwe mukunena.
Pa Wenelatu ndiye pamene aliyense wofika kumene mumzinda wa Blantyre amayambira kuponda. Pamafikatu mabasi a Mafenyetsera, Munorurama, Zvakanedza ndi zina zotere kuchoka ku Bulawayo. Komanso pali basi za ku Joni zimene zimafikira pamene paja. Ndiye tangoganizani munthu wachoka ku Durban, kuthawa kutentha kwa zeno, kudzafika pa Wenela, alipire chimbudzi pomwe komwe adatchonako nzaulere.
Chomwe ndikunena apa n’choti ine monga munthu wamba ndili ndi zofuna zanga pa bajeti.
Chabwino, ngati mukuona kuti ndilibe mphamvu kukambapo za ndondomeko yachuma, mukufuna ndikambe za chiyani? Za kusolola ndi kuphana kudachitika ku kapitolo?
Apo ndangodutsa. Kapenatu mumafuna ndikambe za Baba JT, uja ankatsogolera Male Chauvinist Pig, chipani adatisiyira Gogo uja? Wasowatu mkuluyu.
Kapena ndikambe za Adona Hilida kuti afika liti pano pa Wenela kuchokera kulikonse kumene adapita? Asowatu mayi wathu okondekawa. Kodi nsalu ya paphewa akadakoleka? Nanga komwe aliko akugawanso nkhuku ndi abakha?
Ndili mkati molingalira izi, ndidangoona chigulu cha anthu panyumba ina yomwe ili kuseli kwa Wenela. Ndidapita konko ndipo ndidapeza anthu ali unjiunji.
“Mwamuna wadzigwira yekha ndithu,” ankatero anthuwo.
Kufika pafupi, ndidamva kuti bambo wa m’nyumbayo adatopa ndi mkazi wake ndipo adafuna kuti amusiye basi. Komatu mwamunayo sankamupezera mkaziyo chifukwa.
Adali wachifundo munthu wamayi, wokonda kupemphera, wophika zakupsa, wamalangizo akupsa komanso wodziwa kusamalira mwamuna wakeyo m’njira zonse. Mwamunayo adangotopa naye mkaziyo basi.
Mwamunayo adagwirizana ndi mnzake yemwe ankamwa naye: “Ndikufuna kuti ndimusiye mkaziyu. Njira yabwino ndi yoti ndidzakugwire uli m’magombeza ndi mkazi wanga. Ndatopa naye.”
Winayo adalolera. Ndipo usiku umenewo, winayo adanyamuka msanga kuchoka kumowa. Adalunjika kunyumba yamnzakeyo ndipo adamupeza mkazi wake. Mkaziyo adalola kuti acheze. Koma asanalowe m’magombeza, mkulu uja adapempha kuti avale jekete la mwamuna wa mkaziyo.
Mkazi uja adapereka jekete ndipo nkhani zili mkati, awiriwo atafunda guza limodzi, adangomva kugogoda. Asanaganize chochita, chitseko chidatseguka. Gululu, mwini nyumba wafika.
“Ndiye chiyani ichi Naphi!” adakuwa.
Mwamuna ‘wakuba’ uja adati athawe, koma bambo uja adamuvula jekete. Mbalayo idathawira pakhomo n’kusowa mumdima.
“Lero ndakugwira! Ngakhale mwamuna wakoyo wathawa, ndasunga jekete la kamwamuna kakoko. Umboni wanga kwa ankhoswe. Wagwa nayo basi,” adazaza mwamuna.
“Jekete lili m’manja mwanulo ndi lanu ndiye mukuti umboni wanu uli pati. Kupusa eti. Tangobwerani tizigona apa,” adayankha mayi uja.
Abale anzanga, banja ndi chinthu chofunika, osachitengera chibwana. Inde, iye wapeza mkazi wapeza chinthu chabwino.
Ndipo nkhani ili mkamwa, ndifunire zabwino zonse Paparazzi ndi anzake onse amene amalemba nkhani pomwe akusangalala tsiku lawo pa 3 May.

Related Articles

Back to top button
Translate »