Chichewa

Tadeyo Mliyenda: Polisi Palibe yalowa bwemba

Listen to this article

Tsiku limenelo pa Wenela padavuta zedi. Padafika sing’anga wina adali ndi mitu inayi.
Masalamusiwo adachitika dzuwa likuswa mtengo. Chomwe chidandichititsa chidwi nchakuti mutu ulionse wa mkuluyo adamangapo nsangamutu. Nsangamutu yoyamba idali yachikasu yolembedwa chidule cha Ukafuna Dilu Fatsa ndipo yachiwiri idalembedwa zokhudza NDAba ndekha. Kuona yachitatu, idali chidule cha Male Chauvinist Pigs ndipo yomaliza idali yolemba Polisi Palibe.
“Abracadabra, Abracadabra. Ndine ng’anga Khaki Crossroads, chidule KC ndilibe 2 koloko. Ku Mozambique ndinapita kuja ndabwerako,” idatero ng’angayo.
Kenako idayamba kuimba nyimbo zake zosadziwika bwino. Idayamba kudumpha m’malere ikuloza kumpoto, kudumphanso nkudzaloza kumwera, nkudzadumphanso kuloza kumawa kenako kumadzulo. Imalozatu ndi litchowa lake.
Akamaponda pansi, zingwinjiri za m’mapazi ake zimachita kumveka kuti ngwiririiiiiiiii!
“Ndikumudziwa sing’anga uyu. Tidali limodzi kundende kalelo ndipo ankatithandiza kutulutsa mauthenga ndiye n’chifukwa adali katakwe pofalitsa nkhani. Ndipo nthawiyo adawerenga Baibulo kuchoka Genesis mpaka Chivumbulutso yekha katatu,” adatero Gervazzio.
Abiti Patuma adayankhira: “Zili choncho eti? Nchifukwa chake nthawi ina ankatumikira atapsa, eti?” adafunsa.
Koma maso athu adalunjika kwa Khaki Crossroads, inde KC, mnyamata wa NDAba ndekha. Inde uja adamuuziratu Mpando Wamkulu ndi Ukafuna Dilu Fatsa yake kuti zoima kanayi ayi.
“Ndafika pano pa Wenela kuchotsa ufiti, ufiti wa madyeramphoto. Ndilibe gawo ndi inu a kwakwananda, a nalikonkhwiro, akhwiritontho ndi ananzeze. Mundidziwa bwino. Inetu sindingakhale membala wa gulu la ndale la Economic Freedom Fighters (EFF) lotsogozedwa ndi Julius Malema kutheba,” adali kutero.
Tonse tidadabwa ndi malankhulidwe ake.
“Mtsogoleri wa chipani cha Labour ali ku UK. Mtsogoleri wa EFF ali kwawo ku Joni. Nanga mtsogoleri wa Polisi Palibe, inde Adona Hilida, akhala bwanji kutheba osati pano pa Wenela? Ndatopa nazo,” idali kutero ng’anga ija.
Abale anzanga, ndisaname, sindimadziwa kuti mkuluyo amanena kuti chiyani koma ndidaona onse akuseka.
“Mwatero? Chifukwa chakuti Adona Hilida akupitiriza kubisala kunja ndiye basi mwati muwataye? Osawaitanitsa bwanji? Masiku apitawa tidamva kuti Harry Porter komanso uja mnyamata wachichepere ankatiuza kuti amadziwa masamu zedi ndipo adawerengera kuti Adona Hilida ndiye chiwongolero naye wazitaya! Kodi mukhazikitsa magulu angati akulu? Zoti mudatha simungavomereze nkupita ku Chisitu kukatchola tiyi?” adafunsa.
KC adapukusa litchowa.
“Ine palibenso. Ndimachokera kuzitsamba ku Mulanje ndikhoza kukusandutsa mwamuna, ndisamale. Kodi sudziwa palibenso akadatha Mpando Wamkulu koma ine?” adatero KC.
“Zonse zili apo, Polisi Palibe ikutha ngati makatani, sitiikira chigamba. Nayo Ukafuna Dilu Fatsa ikuyenda msewu womwewo. Hamba naweeee!” adatero Abiti Patuma.
Abale anzanga, tiyeni tivomereze, galimoto ya Anglia Bonono idatha kale. Sitingaikemo injini ya BMW!
Gwira bango upita ndi madzi iwe!

Related Articles

Back to top button