Nkhani

Takana kupha makanda

Listen to this article

Ife sitivomera kupha makanda.” Uwu ndi uthenga womwe aphungu a Nyumba ya Malamulo auza Tamvani kuti aombera bilo yopatsa mwayi amayi kuchotsa pathupi ikatera m’nyumbayo.

Tamvani m’sabatayi idalankhula ndi aphungu 141 mwa aphungu 188 amene alipo m’dziko muno.

Aphungu akuti bilo yochotsa mimba ayi: Mayi wapakati ku Chileka

Mwa 141, aphungu 113 anenetsa kuti biloyo ikafika m’nyumba ya Malamulo kuti aikambirane, iwo sayerekeza kulola kuti biloyo idutse kukhala lamulo.

Pamene aphungu 26 akuti sadapange chiganizo pa zomwe akachita biloyo ikakafika m’nyumbayo. Aphungu awiri okha ndiwo avomera kuti akalola biloyo kuti idutse.

Aphungu amene akana kuvomera kuti biloyo idutse akuti ndi bwino akapsere zina kumwamba osati chifukwa choti avomereza amayi ndi atsikana kuchotsa pakati.

“Kumenekotu ndi chimodzimodzi kupha kumene. Ineyo monga mkhristu sizoona kuti ndikavotere zimenezo,” adatero Ireen Mambala phungu woima payekha m’boma la Balaka.

Naye Gertrude Nankhumwa ya Blantyre Kabula akuti moyo amapereka ndi Mulungu ndipo Mulungu yekha ndiye ali ndi mphamvu yochotsa.

Susan Ndalama wa ku Blantyre Rural East akuti anthu sadaphunzitsidwe mokwanira zomwe zili mu biloyo komwe kukhale kovuta kuti avomereze.

Phungu wa Mzimba East, Wezzie Gondwe adati ngakhale iye akuvomereza biloyo komabe kukhala kovuta kuti akailole idutse chifukwa anthu a dera lake amakhulupirira kuti kuchotsa pakati ndi tchimo.

Kamlepo Kalua wa ku Rumphi East adati kuvomera biloyo kuli ngati kuwalola anthu kuti atha kumaphana.

“Sindingavomereze biloyo, ndipo sindidzavomerezapo. Kuli ngati kulola kuti tidziphana, ndiye dera langa izi ayi,” adatero Kalua.

Francis Phiso wa kummwera kwa boma la Blantyre komanso Thoko Tembo wa kummwera kwa boma la Neno adati akudikira kaye kuti awerenge bwino biloyo komanso amve maganizo a anthu awo.

Amabungwe ali ndi lingaliro lobweretsa biloyo m’nyumba ya Malamulo pamene aphungu akhale akukumana kuti akaikambirane.

Lingaliro lofuna kubweretsa biloyo lakwiitsa amipingo komanso amabungwe ena amene akupempha aphunguwo kuti asalole kuvomereza kuti biloyo idutsa kusanduka lamulo. n

 Atolankhani awa athandizira, Angela Phiri, Fatsani Gunya, Lucky Mkandawire, Suzgo Chitete ndi Joseph Mwale.

Related Articles

Back to top button
Translate »