Nkhani

Takonzeka kuvota—Amalawi

Listen to this article

Pamene kwangotsala masiku awiri kuti Amalawi 6.8 miliyoni aponye voti yosankha mtsogoleri wa dziko lino, Amalawi ena asonyeza chidwi kuti akonzeka kukavota Lachiwiri.

Tamvani idazungulira kuona momwe anthu akukonzekera ndipo ena aonetsa kuti Lachiwiri adzakhala pikitipikiti kukaponya voti.

“Apapa ngakhale atasintha kuti votiyo ikhale lero, ndipita kukavota ndipo sindikulira wina kupanga kampeni paine chifukwa chisankho ndidapanga kale,” adatero MacDonald Kalimba wa ku Mchinji.

Joel Ngoma wa ku Mzimba adati: “Chomwe ndimadikira ine n’choti tidzavota liti ndiye poti tsiku likudziwika, ndikungondikira mmawa wa Lachiwiri basi kukavota.”

Amayi nawo ati akonzeka kukaponya voti Lachiwiri kuti dziko la Malawi likhale ndi mtsogoleri wovomerezeka.

“Tonse tikudziwa kuti zinthu zambiri zidaima chifukwa cha ndalezi ndiye mpofunika kuti Lachiwiri lifike msanga kuti mtsogoleri adziwike tiyambe kusuntha chitsogolo,” adatero Shupekile Mlotha wa ku Karonga.

Pomwe Patuma Usumani wa ku Phalombe adati: “Tidavota koma pazifukwa zina akuti tikavotenso ndiye likafika tsikulo tikavota kuti tikhazikike. Izi zokokanakokana sizitithandiza.”

Nalo bungwe lophunzitsa anthu la National Initiative for Civic Education (Nice) Trust lati lazungulira dziko lonse kuphunzitsa anthu zakavotedwe ndipo likukhulupilira kuti anthu akavota mwaunyinji.

Mneneri wabungwelo Grace Hara wati bungwelo lidamwaza mauthenga m’njira zosiyanasiyana kuti Amalawi ngakhale akumudzi kwambiri amve za chisankho cha mkujachi.

“Ulendo uno, ndi bungwe lathu lokha lomwe lidali kalikiliki kuphunzitsa ndi kumema anthu zachisankhochi kupatula zipani zomwe zomamemanso anthu. Chokondweretsa n’choti anthu akuonetsa kuti alandira uthenga mokwanira,” adarero Hara.

Kadaulo pa kayendetsedwe ka zinthu m’dziko Vincent Kondowe wati chisankho ndi chimenecho koma chofunika ndi umunthu kuti zinthu zidzayende bwino.

Iye wati munthu aliyense akuyenera kuzindikira kuti ufulu wake wokaponya voti ndi ufulu wa anthu enanso choncho ndi bwino kuti aliyense Lachiwirilo akaponye voti yake akathana nazo n’kumapita kwawo kukadikira zotsatira.

“Amalawi apite mwaunyinji kukavota chifukwa voti yawo ndi tsogolo lawo ndi la ana awo koma aliyense adzatsogoze umunthu osati kudzikonda ayi. Timanena nthawi zonse kuti dzikoli ndi lathu ndipo olichengetera ndife tomwe,” adatero Kondowe.

Kadaulo pandale George Phiri wati Amalawi adapanga kale chiganizo cha kavotedwe koma adati mpofunika kuti asankhe mtsogoleri yemwe wawauza mfundo zomveka pakampeni kuopa kudzagwira fuwa lamoto.

“Munthu wofuna voti amayenera kupanga kampeni kuuza anthu zomwe wakonza. Kungovotera kuti ndakonda uyu, mawa podzafunsa zitukuko amadzati ‘N’nalonjeza liti’? Anthu basi kakasi,” adatero Phiri.

Kwa atsogoleri omwe akudzaima nawo, Phiri wati potengera malamulo, kampeni ikuyenera kutsekedwa mawa Lamulungu 6 koloko mmawa ndiye akuyenera kuti atsindika mfundo zawo moyenera.

Iye wati voti ya Lachiwiri ndi mwayi wachiwiri kwa Amalawi kusankha mtsogoleri wakum’tima kotero akuyembekeza kuti Amalawi akavota mwaunyinji.

Wampando wa bungwe la Malawi Electoral Commission (MEC) Chifundo Kachale adauza atolankhani sabata yatha kuti bungwelo ndi lokonzeka kuyendetsa chisankhocho ngakhale palo mavuto ena.

Vuto lalikulu lomwe lolipo ndikupelewera kwa ndalama ndi K7.8 biliyoni pa bajeti yonse ya chisankho.

Potengera zipsinjo zomwe zidaoneka pa kampeni, mneneri wa polisi James Kadadzera wati apolisi adzaonetsetsa kuti aliyense wavota mwamtendere Lachiwirilo.

“Takhala tikupereka chitetezo ku zipani zonse pa kampeni. Tipitirira mpaka anthu avote komanso tidzapitirira kuteteza anthuwo,” adatero Kadadzera.

Chisankhochi chichitika chifukwa khoti lidapeza kuti chisankho cha mtsogoleri wa dziko cha 2019 sichidayende bwino potsatira dandaulo la Lazarus Chakwera wa MCP ndi Saulos Chilima wa UTM omwe akupita kuchisankhochi pa mgwirizano.

Pachisankhochi, apikisane ndi m’gwirizano wa MCP ndi UTM komanso zipani zina zisanu nziwiri ndipo mgwirizanowo akuutcha Tonse Alliance ndipo mgwirizano wa DPP ndi UDF komanso Mbakuwaku Movement for Development (MMD).

Chakwera akuimilira Tonse Alliance, Peter Mutharika akuimira mgwirizano wa DPP ndi UDF pomwe Peter Kuwani akuimira MMD.

Related Articles

Back to top button