Chichewa

Tame Mwawa: Phwete ndiye kudya kwake

Listen to this article

 

Sewero la Tikuferanji ndi limodzi mwa masewero omwe amapereka phunziro kwa anthu pazochitika m’moyo wa tsiku ndi tsiku komanso ndi msangulutso kwa anthu ambiri. Seweroli limaonetsedwa pakanema komanso kumveka pawailesi ya MBC. STEVEN PEMBAMOYO adachita chidwi ndi mmodzi mwa omwe amachita nawo seweroli, Tame Mwawa, yemwe ambiri amamudziwa kuti Chiphwanya museweromo ndipo adacheza naye motere:

Mwawa: Ndidabadwa wazisudzo
Mwawa: Ndidabadwa wazisudzo

Ndikudziwe mnzanga.

Ndine Tame Mwawa ndimakhala ku Machinjiri ku Blantyre koma kwathu nku Chiradzulu m’mudzi mwa Kambalame, T/A Mpama.

Udabadwa m’chaka chanji?

Ndidabadwa pa 26 October, 1977 ndipo ndine woyamba m’banja la ana 7, amuna 5 ndi asungwana awiri.

Mbiri yako pazisudzo ndi yotani?

Ndikhoza kunena kuti ndidabadwa wazisudzo kale. Abale anga amandiuza kuti ndili wamng’ono ndikadziongola kapena ndikamalira anthu amandiunjirira n’kumaseka ndipo makolo anga adadziwiratu kuti ndidzakhala msangalatsi. Kusukulu anzanga ngakhalenso aphunzitsi ankachita kudziwa kuti Tame wabwera zilango ndiye zidali zosatha. Nthawi zina ndinkalembedwa pa anthu olongolola koma pomwe sindidapite kusukulu n’komwe. Pachikondwerero chokumbukira ufulu wa dziko ndinkapanga nawo zisudzo ndipo malipiro ake adali Fanta ndi mpunga wa nyama. Ndinkapanganso sewero la Ambuye Yesu.

Udapezeka bwanji musewero la Tikuferanji?

Nthawi ina yake ankakajambula seweroli pafupi ndi kwathu ndiye penapake pamafunika sing’anga koma munthu amasowa tsono ine ndidadzipereka kuti ndiyesere nkuchita bwino basi kulowa mseweroli kudali kumeneko. Panthawi imeneyo ndidadziwana ndi akuluakulu ena azisudzo monga Frank Yalu (Nginde) yemwe adanditenga kukalowa gulu lake la zisudzo lotchedwa Kasupe Arts Theatre. Pano ndidadziwika kwambiri moti ndimapezeka m’magulu azisudzo osiyanasiyana monga Kwathu komanso mumafilimi osiyanasiyana. Imodzi mwa mafilimu omwe ndilimo ndi ya Ching’aning’ani yomwe ikuoneka pakanema ya Malawi komanso ndidayambitsa nawo pologalamu ya Phwete pa kanema yomweyi. Pawayilesi ndimapanga nawo Sewero la Sabata Ino.

Dzina la Chiphwanya lidayamba bwanji?

Kumudzi kwathu ku Chiradzulu kuli mkulu wina dzina lake Chiphwanya yemwe ndi wolongolola komanso wosachedwa kupsa mtima ndiye nditaona malo omwe ndimapatsidwa m’masewero ambiri ndidaona kuti dzinali ndi londiyenera.

Nzoona kuti pakhomo pako udadzala zikho zambiri?

Eya, ndimadziwiratu mbali zomwe anzanga amakonda kundipatsa pazisudzo motero ndidadzala zikho zambiri komanso mikanda pakhomo panga ili mbweee! Moti anthu ena amaona ngati ndimapangadi zausing’anga.

Nanga mano adaguluka nchiyani?

Munthune ndimavutika ndi mutu kwambiri moti umati ukandimenya mano angapo amayenera kuchoka basi. Bambo anganso n’chimodzimodzi moti iwo mano awo ammwamba adatha onse. n

Related Articles

Back to top button