Chichewa

Taphulanji m’zaka 52?

Listen to this article

 

Anthu komanso atsogoleri ena ati zaka 52 za ufulu wodzilamulira zomwe dziko la Malawi lidakwanitsa Lachitatu ndi nthabwala chabe chifukwa zinthu zanyanya kusiyana ndi kale.

Anthuwa amalankhulapo kumbali ya momwe ndale zikuyendera, chuma, maphunziro komanso ulamuliro wabwino m’zaka 52 zomwe zapita.

Mkulu wa bungwe loona zamaphunziro la Civil Society Education Coalition (CSEC) Benedicto Kondowe wati zomwe Malawi wakwaniritsa m’zaka 52 kumbali ya maphunziro, maiko ena azichita m’zaka 20 zokha.

Iye wati kumudzi komwe kumakhala anthu ambiri, zinthu sizili bwino ngakhale tikusangalala kuti takwanitsa zaka 52 zodziyimira patokha.

“Pitani ku Chikwawa, sukulu zina kuyambira sitandade 1 mpaka 8 ana ali ndi mphunzitsi mmodzi. Pitani ku Dedza, mphunzitsi mmodzi akuphunzitsa ana 400. Zomwezi mukazipezanso ku Rumphi.

Amalawi kulimbirana chimanga nthawi ya njala
Amalawi kulimbirana chimanga nthawi ya njala

“Ana akuphunzirabe pansi pa mitengo apo ayi ndiye kuti ndi m’chisakasa chomwe makolo amanga. Kodi izi zikutanthauzadi kuti takwanitsa zaka 52?” adafunsa Kondowe.

Iye adati ku Angola, mphunzitsi mmodzi akuphunzitsa ana osaposa 45 pamene ku Malawi mphunzitsi mmodzi akuphunzitsa ana oposa 100 zomwe wati maphunziro akulowa pansi mmalo moti asinthe.

“Ku Mozambique, Zambia ngakhale Zimbabwe, sitingafanane nawo. Ndikuchokera ku Machinga komwe ndidaona mphunzitsi akuphunzitsa ana oposa 400 yekha. Kodi zaka 52 zili ndi tanthauzonso pamenepa?” adazizwa Kondowe.

Iye adati chomwe angaloze kumbali ya maphunziro ndi chiwerengero cha ana amene akupita kusukulu komanso kupezeka kwa sukulu m’madera ambiri zomwe ndi nkhani yabwino.

Kumbali ya ndale, mphunzitsi wa ndale kusukulu ya Chancellor Collage Joseph Chunga wati palibe chomwe angaloze koma mavuto okhaokha.

Ngakhale Chunga akuti palibe angaloze, dziko lino lili ndi zipani zambiri zoposa 50 pamene kale kudali chipani chimodzi chokha.

“Izi si zoti mungamaloze kuti ndale zikuyenda bwino chifukwa tili ndi zipani zambiri. Ndikutero chifukwa mukadzifunsa mupeza kuti zipanizo zikuyambidwa chifukwa cha kusamvana komwe kwabuka m’chipani ndipo mulibe kulolerana, mapeto ake ndi kukayambitsa chipani chawo. Ndiye uku ndi kutukuka?

“Komanso ngakhale zipanizo zikufika 50, ndi zipani zingati zomwe zikuoneka? Mupeza kuti nzosaposa zisanu,” adatero Chunga.

Iye adaonjeza kuti dziko la Malawi adati mlozo wina kuti zinthu sizikuyenda pa ndale zikuonekera pomwe mtsogoleri akangochoka pampando, umakhala ulendo wa mchitokosi.

Poyankhapo pa momwe zinthu zikuyendera m’dziko muno, womenyera ufulu wachibadwidwe, Billy Mayaya wati atsogoleri athu ndiwo asokoneza zinthu kotero akuyenera kuchotsedwa.

Iye wati mavuto akhodzokera ndipo mmalo mopita patsogolo, zinthu zikubwerera mmbuyo, zomwe wati zikuchitika chifukwa cha atsogoleri.

“Dziko limayenda bwino ngati anthu akupeza mwayi wa ntchito, anthu akukhala ndi ndalama komanso ngati anthu akukwezeredwa ndalama m’malo amene akugwirira ntchito. Izi m’dziko muno ndi vuto lalikulu, ntchito zikusowa komanso anthu sakukwezeredwa malipiro.

“Zinthu zasokonekera ndipo zonsezi ndi atsogoleri amene tidawasankha kuti akonze zinthu, ndiye ngati zinthuzo sizikukonzedwa, ndi bwino kuwachotsa kuti pabwere ena amene angatithandize,” adatero Mayaya.

Kunyadira ufulu wodzilamulira

Dziko la Malawi lidalandira ufulu wodzilamulira pa 6 July 1964 kuchokera ku ulamuliro wa atsamunda a Chingerezi. Lachitatu lapitali, timakumbukira kuti patha zaka 52 kuchokera pomwe tidayamba kudzilamulira. STEVEN PEMBAMOYO adacheza ndi mikoko yogona Moses Malunga ndi Mustaf Mbewe za mbiri ya ufulu wathu. Adacheza motere:

Ndiyambe ndi inu bambo Mbewe, 6 July imatanthauzanji pa mbiri ya Malawi?

Tsikuli ndi lokumbukira kuti dziko la Malawi lidatuluka mmanja mwa ulamuliro wa Angerezi omwe ankadziwika kuti atsamunda. Kalelo Amalawi adalibe mphamvu iliyonse pa kayendetsedwe ka dziko koma kumangotsatira zomwe azunguwo ankafuna kufikira pomwe ulamuliro wawo udagwetsedwa. Tsikuli lili ngati chikumbutso chabe koma ndi tsiku lofunika pa mbiri ya dziko la Malawi.

Kodi kalelo zimakhala bwanji pokumbukira tsiku limeneli?

Sizisiyana kwenikweni ndi momwe zimakhalira masiku ano kungoti panopa zidakhala ngati zidakhwepa pang’ono. Kalelo, kunkakhala galimoto zonyamula ana a sukulu kupita nawo kubwalo la chikondwerero komanso lidali tsiku lolemekezeka. Pano si anthu amatha kukagwira ntchito zawo tsiku ngati limeneli? Kale kudalibe zoterezi.

Mukati tsikuli layenda bwino mumaonera chiyani?

Choyambirira ndi tchuthi. Anthu samapita kuntchito ngakhale ganyu komanso mbendera ya Malawi imakhala petupetu mmalo osankhidwa. Uku kumakhala kusonyeza kuti kwachadi ku Malawi, chitsimikizo choti anthu ayera mmaso ayamba kudzilamulira. Zambiri zimachitika monga zionetsero zosiyanasiyana, mapemphero ndi masewero. Aliyense amakhala okondwa ndi wa chimwemwe.  Asilikali a nkhondo nawo amakhala ndi chionetsero chawo kusangalatsa anthu ndipo mtsogoleri wa dziko amalankhula mawu a chilimbikitso ku mtundu onse. Omwe adali nkuthekera amatha kupanga maphwando m’nyumba zawo.

Nanga momwe zimakhalira masiku ano mumaona bwanji? Cholinga cha tsikuli chimakwaniritsidwa?

Tingaterobe poti nanga si anthu amakhala akukumbukira ufulu odzilamulira koma aaàa,  pena pake pamacheperabe. Kalelo kukonzekera kumayamba masiku angapo tsiku lenileni lisadafike.

Nanga inu a Malunga tiuzeni za mbiri ya tsikuli.

Tsikuli lidakhazikitsidwa pafupifupi zaka 52 zapitazo m’boma la chipani chimodzi kuti anthu azikumbukira momwe adalandirira ufulu odzilamulira okha. Kunena zoona, pomwe zidafika zinthu nthawiyo m’manja mwa atsamunda, kudali kofunika kuti ufulu ngati umenewu uperekedwe.

Mukutanthauzanji pamenepo?

Akuyamba kuimba ndi zaka 5 pano kudalibe. Anthu akuda eni nthaka ankakhala ndi malire m’dziko mwawo momwemuno, padali malo ena omwe munthu wakhungu lakuda  samaloledwa kufikako chabe chabe ndipo akamati ufulu udali m’manja mwa anthu obwera zidalidi zowona. Mabizinesi ndi ma esiteti akuluakulu adali mmanja mwa azungu ndipo anthu akuda adali a ntchito chabe.

Nanga poti ena amati kutenga ufuluwu kudasokoneza chitukuko inu mungatiuze zotani?

Kumvetsa ndi kutanthauzira nkosiyana. Omwe adakhalako mu ulamuliro wa atsamunda adzakuuzani zina ndipo ena omwe akugwiritsa ntchito maphunziro potanthauzira zinthu adzakuuzani zina. Sindikuuzani maganizo anga koma ndikufusani funso lomwe Amalawi ena ofuna ayankhe pawokhapawokha. Chabwino nchiti kukhala m’chitukuko chomwe sungadyerere nawo nkumalimbikira movutika wekha kuti uzisangalala? Muyankhe nokha mumtima.

Taunikirani bwino pakusiyana kwa moyo wa masiku ano odzilamulira ndi moyo wakale wa mmanja mwa atsamunda.

Moyo umakoma ndi  ufulu kulikonse. Mudzaone munthu wachuma yemwe ali ndi ngongole zambiri ndi munthu osauka yemwe  akudya zochepetsa zomwe alinazozo, amaoneka osangalala ndani? Ufulu ndi ufulu kulikonse palibe kuti ukukhala kapena kugona potani koma ngati uli mfulu ndiwe munthu. Kwa ine bola pano chifukwa Amalawi ali ndi malo olimapo, okhalapo komanso ali ndi mphamvu zopanga malamulo oyendetsera dziko okha umenewu ndiye timati mtendere. Inu simungakhale ndi banja nkumayembekezera kuti wina wake abwere nkumakuuzani zoti muchite ndi momwe mungayendetsere banjalo.  Umu ndimo zidalili kalero.

Related Articles

One Comment

  1. Iwe Kabango: Nkhani iyi yatalika kwammbiri!
    Anthu amene timawerenga nkhani m’chichewa, m’mizi muno, timawerenga kwenikweni chifukwa sitimawerenga chizungu bwino, Ndipo tilibe nthawi yoti tiwerenge nkhani yotalika chonchi; pamene ukanena zonzeso ndi katalikisako kugawa patatu (1/3) baasi! Aaaaaaaa!

Back to top button