Nkhani

‘Tataya nanu chikhulupiriro’

Listen to this article

Kwayaka moto! Zipani zina zotsutsa zati zilibenso chikhulupiriro ndi mkulu wa bungwe loyendetsa chisankho la Malawi Electoral Commission (MEC) Jane Ansah ndipo amupempha kuti achoke.

Izi zimalankhulidwa ku msonkhano wa National Elections Consultative Forum (Necof) womwe udachitikira ku Lilongwe Lachitatu m’sabatayi kutsatira mpungwepungwe womwe wabuka ku MEC.

Msonkhanowo umachitika kutsatira kusowa kwa makina amene MEC imagwiritsira ntchito potolera maina a anthu amene adzavote mu May 2019 komanso kompiyuta.

Pamsonkhanowo, zipanizo zidapempha kuti papezeke akadaulo apadera kuti afufuze bwinobwino nkhani yokhudza kusowa kwa makinawo amene adapezeka m’dziko la Mozambique koma kompiyuta sidapezekebe.

Koma Ansah adatsutsana ndi ganizo la azipani komanso amabungwe amene adali pamsonkhanowo.

“Sindikuona chifukwa chimene tikuyenera kupezera akadaulo kuti adzafufuze,” adatero Ansah.

Iye adati pamene makinawo amasowa n’kuti bungwelo litachotsa kale uthenga womwe adatolera kutanthauza kuti kusowa kwa makinawo sikudasokoneze chilichonse.

Izi zidakwiyitsa zipani. Mthumwi ya chipani cha PP, Ibrahim Matola adadzudzula Ansah kuti nkhaniyo akuitengera chibwana.

“Timayenera kuuzidwa pamene izi [makinawo atasowa] zitangochitika, ndiye chomwe tikuona n’kuti nkhaniyi mukuyitengera chibwana ndipo n’chifukwa tikuti mutule pansi,” adatero Matola.

Mkulu wa achinyama m’chipani cha MCP, Richard Chimwendo Banda adati pa nkhaniyo palibe kukambirana koma MEC ivomereze kuti pabwere akadaulo apadera kuti achite kafukufuku.

Naye mneneri wa gulu la chipani la United Transformation Movement (UTM), Chidanti Malunga adati achotsa chikhulupiriro chawo mwa MEC malinga ndi zomwe zikuchitika ku bungwelo.

“Nkhani sizikutha ku bungweli, nthawi zonse kukumamveka nkhani zomwe zingachotse chikhulupiriro cha anthu kuti adzavote. Ife tikutsatira zomwe zikuchitikazo ndipo posakhalitsa titulutsa kalata ya zomwe zichitike,” adatero Malunga.

Mkulu wa bungwe la Malawi Electoral Network Support Network (Mesn), Steve Duwa adati chikufunika n’kuti pabwere akadaulo amene afufuze kubungwelo.

“Anthu komanso zipani zimayenera zikhale ndi chikhulupiriro mwa MEC yomwe ikuyendetsa zisankhozi. N’chifukwa pakufunika kuti akadaulo afufuzeko ndipo mtima wa aliyense udzakhala mmalo,” adatero Duwa.

Related Articles

Back to top button
Translate »