Chichewa

TB ya kumsana imapha ziwalo

Listen to this article

 

Dokotala wothandiza anthu omwe ali ndi vuto la kufa kwa ziwalo kuchipatala cha Kachere Rehabilitation Centre mumzinda wa Blantyre, Veronica Mughogho, wati TB ya kumsana   imapha ziwalo.

Iye  adati padakalipano,  ambiri mwa anthu omwe akumabwera kudzalandira thandizo kubungweli,  gwero lake likumakhala TB ya kumsana yomwe imatchedwa spinal TB m’Chingerezi.

“Zikuoneka kuti ambiri sakuyidziwa n’chifukwa chake anthu amapita kuchipatala mochedwa zinthu zitafika kale poipa,” adatero iye.

Masewero ngati awa amathandiza ziwalo ziyambenso kugwira ntchito

Mughogho adati nthendayi imayamba pang’onopang’ono ndi kupweteka kwa msana ndipo munthu amanyengeka ndi kumangomwa mankhwala opha ululu.

“Kupweteka kwa msanaku kumapitirira kwa nthawi yaitali ndipo ululu wake umachulukira. Munthu akaona kuti wakhala nthawi yotalikirapo akumva ululuwu, akuyenera kukayezetsa mwamsanga kuti alandire thandizo mwamsanga zinthu zisanafike poipa monga kufa ziwalo,” adatero dokotalayu.

Iye adati zizindikiro zina ndi monga kumva kuzizira, kutuluka thukuta usiku, kuonda komanso kutuluka chotupa pantchafu. Adaonjeza kuti tizilombo tomwe timayambitsa nthendayi ndi tofanana ndi tomwe timayambitsa TB ya m’mapapo yomwe imadziwika kuti chifuwa chachikulu.

“Kusiyana kwake n’kwakuti tizilomboti timakhamukira kumsana ndi kumadya nyama ndi fupa la kumsanandipo mafinya amayamba kutuluka ndipo amalowa mkati mwa msana ndi kufinya mtsempha waukulu umene umalumikiza uthenga kuchokera kubongo kupita ku ziwalo zina za thupi,” adatero Mughogho.

Iye adaonjeza kuti izi zikapitirira, mtsemphawo umatha kuduka ndipo zosatira zake zimakhala kufa kwa mbali ya thupi kuchokera pomwe padukapo, kupita kumunsi.

Mughogho adati ngati TB yazindikiridwa munthu atafa kale ziwalo, munthuyo amalandira thandizo la mankhwala kenako amatumizidwa ku malo ochitirako masewero.

“Ziwalo zimatha kuyambiranso kugwira ntchito ngati mtsemphawo siunaonongeke kwambiri koma ukaonongekeratu, munthu amalumala mpaka kalekale. Ndi chifukwa chake tikuti anthu akuyenera kukayezetsa akayamba kuona zizindikirozi kuti alandire thandizo la mankhwala mwa msanga,” adatero dokotalayu.

Iye adati TB ya m’mapapo imadziwika mwamsanga chifukwa munthu amakhosomola pamene,TB ya kumsana munthu sakhosomola. n

Related Articles

Back to top button