Chichewa

Tetezani kukokoloka kwa nthaka ndi biyo

Listen to this article

 

Njira zotetezera nthaka kumadzi othamanga zili mbwee, koma katswiri wa zanthaka kusukulu yaukachenjede ya Chancellor College, Dr Jimmy Namangale, wati kuika biyo m’malo momwe mumadutsa madzi ndi njira yabwino yopewera ngalande m’munda.

Polongosolera Uchikumbe sabata ino, katswiriyu adati mmalo momwe mumadutsa madzi, makamaka m’munda, zaka zikamapita mumasanduka ngalande kutanthauza kuti nthaka yomwe idali pamenepo idanka kwina ndi madziwo.

Iye adati mlimi akalekelera osachitapo kanthu, zotsatira zake munda umaonongeka komanso zimachititsa kuti mitsinje ndi madambo omwe amasunga madzi omwe akadagwira ntchito ya mthirira zikwiririke.

Biyo wopangidwa ndi miyala amateteza nthaka ku madzi othamanga
Biyo wopangidwa ndi miyala amateteza nthaka ku madzi othamanga

“Ili ndi limodzi mwa mavuto omwe alimi ambiri amalekerera koma ndi chifukwa chimodzi mwa zifukwa zomwe zabwezeretsa ulimi mmbuyo. Zimaoneka ngati palibe chomwe chikuchitika chifukwa chaka chilichonse gawo lochepa lokha la nthaka ndilo limapita.

“Izi zimakhala zikuchitika chaka ndi chaka ndipo podzazindikira, m’munda mumakhala mutadzadza ngalande ngati mitsinje,” adatero Namangale.

Katswiriyu adati njira yodalirika yopewera zoterezi n’kuyika biyo m’malo momwe mumadutsa madzi kuti liwiro la madzi oyendawo lizichepa komanso biyo amathandiza kuwakha nthaka yomwe imayenda ndi madzi.

Paupangiri wake, iye adati biyo savuta kukonza kwake, koma n’zoyenerera kufunsa upangiri wa alangizi pogwira ntchitoyi chifukwa pamakhalanso ukadaulo wapadera kuti miyala yopangirayo ilimbe, isadzakokoloke.

“Biyo amateteza nthaka ku madzi oyenda, makamaka othamanga, monga mudziwa kuti masiku ano mvula ikangogwa pang’ono madzi amathamanga kwambiri chifukwa chosowa poimira malingana nkuti mitengo ndi chilengedwe zidatha,” adatero Namangale.

Mkuluyu adati pokhapokha mavuto ngati awa atathetsedwa, ngozi zina ngati kusefukira kwa madzi ndi kukokoloka kwa mbewu zisanduka nyimbo ya chaka chilichonse komanso nthaka idzafika potheratu kutsala thanthwe basi.

Mogwirizana ndi zimene adanena Namangale, katswiri wina wa zanthaka ku Bunda, Dr Patson Nalivata, adati pomwe alimi akuyesayesa njira zosiyanasiyana zobwezeretsera chonde m’nthaka, mpofunikanso kuti azitsatira njira zoteteza kukokoloka kwa nthakayo.

Iye adati palibe tanthauzo lililonse kuti chaka ndi chaka alimi azikhala ndi ntchito yokokera chonde m’manyowa koma osachiteteza kuti chisakokolokenso.

“Ngakhale pankhani za umoyo zenizenizi amati choyambirira n’kupewa kenako kuchiza pambuyo zikavuta. N’chimodzimodzi nthaka imafunika kuiteteza kuti isakokoloke. Zikavutitsitsa ndiye kumalimbana ndi kubwezeretsa chonde,” adatero Nalivata.n

Related Articles

Back to top button
Translate »